settings icon
share icon
Funso

Munalandira Moyo Wosatha?

Yankho


Baibulo limatipatsira njira yosavuta yopita kumoyo wosatha. Poyamba, tizindikire kuti tachimwira Mulungu: “pakuti aliyense anachimwa ndikutalikira ulemelero wa Mulungu” (Aroma 3:23). Tonse tapanga zinthu zokhumudwitsa Mulungu, zimene zitipangitsa kulandira chilango. Pachifukwa chakuti machimo athu onse ndi wochimwira Mulungu kotheratu, ndi chilango chosatha chokha chimene chili chokwanira. “Mphotho yake ya uchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu” (Aroma 6:23).

Komabe, Khristu Yesu, amene sanachita tchimo (1 Petro 2:22), mwana wake wa muyaya wa Mulungu anakhala munthu (Yohane 1:1,14) ndipo anafa kutipulumutsa ife kumachimo athu. “Mulungu amaonetsa chikondi chake kwa ife mu ichi: pamene tidakali wochimwa, Khristu anatifera ife” (Aroma 5:8). Yesu Khristu anafa pamtanda (Yohane 19:31-42), kutenga chilango chimene chinali cha ife (2 Akorinto 5:21). Patatha masiku atatu anawuka kwa akufa (1 Akorinto 15:1-4), kutsimikizira ukulu wake pa tchimo ndi imfa. “M’chisomo chake chachikulu anatibalanso mchiyembekezo cha moyo kudzera mu kuukanso kwa akufa kwa Yesu Khristu.” (1 Petro 1:3)

Mwa chisomo, tisinthe maganizo athu pa Khristu – kuti Iye ndani, zimene anachita, ndi chifukwa – kuti tipeze chipulumutso (Machitidwe a Atumwi 3:19). Ngati tiyika chikhulupiliro chathu mwa Iye, kukhulupilira imfa yake pa mtanda kutiombola kumachimo athu, tidzakhululukidwa ndikulandira lonjezo la moyo wosatha kumwamba. “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero anapatsa mwana wake obadwa yekha Ambuye wathu, kuti yense wakukhulupilira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha (Yohane 3:16). “Ngati udzabvomereza ndi kamwa yako, kuti ‘Yesu ndi Ambuye,’ ndi kukhulupilira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka” (Aroma 10:9). Chikhulupiliro chokha mu ntchito yokwaniritsidwa ya Khristu pa mtanda ndiyo njira yokhayo yoona ya kumoyo wosatha! “Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo, mwa chikhulupiliro – ndipo ichi chosachokera kwa inu, chili mphatso ya Mulungu – chosachokera ku ntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.” (Aefeso 2:8-9)

Ngati mufuna kulandira Yesu Khristu kukhala Mpulumutsi wanu, ili ndi pemphero longoyerekeza. Kumbukirani, kunena pemphero ili kapena pemphero liri lonse sikungakupulumutseni. Ndikukhulupilira mwa Yesu kokha kumene kungakupulumutseni ku machimo. Pemphero ili ndilongosonyeza kwa Mulungu chikhulupiliro chanu mwa Iye ndikumuthokoza pakukupatsani za chipulumutso chanu. “Mulungu, ndikuzindikira kuti ndakulakwirani ndipo ndili oyenera chilango. Koma Yesu Khristu anachitenga chilango chimene chinali choyenera ine kotero kuti mwa chikhulupiliro mwa Iye ndikhonza kukhululukiridwa. Ndikuyika chikhulupiliro changa mwa inu kuti ndikapulumuke. Zikomo chifukwa cha chisomo chanu chodabwitsa ndi kukhululuka kwanu – mphatso ya moyo osatha! Amen!”

Kodi mwapanga ganizo la Khristu chifukwa cha zimene mwawerenga pano? Ngati ndi choncho, chonde sindikizani batani la “Ndavomera kulandira Khristu lero” pansipa.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Munalandira Moyo Wosatha?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries