settings icon
share icon
Funso

Ndangoyika chikhulupiliro changa mwa Yesu… Tsopano?

Yankho



Ndangoyika chikhulupiliro changa mwa Yesu… Tsopano?

Takuyamikani! Mwapanga ganizo labwino losintha moyo! Mwina mukufunsa, “Tsopano? Ndiyambira pati ulendo wanga ndi Mulungu?” Magawo asanu amene atchulidwa pansipa akusonyezani njira kuchokera mu Baibulo. Pamene muli ndi mafunso pa ulendo wanu, chonde pitani ku: www.GotQuestions.org/Chichewa.

1. Onetsetsani kuti mukudziwa za chipulumutso.

1 Yohane 5:13 akutiuza kuti, “Izi ndakulemberani kuti mudziwe kuti muli ndi moyo osatha.” Mulungu akufuna ife tidziwe za chipulumutso. Mulungu akufuna ife tikhale ndi chikhulupiliro chodziwa bwinobwino kuti tapulumutsidwa. Mwachidule, tiyeni tipite kumitu ya chipulumutso:

(a) Tonse tinachimwapo. Tonse tinachitapo zinthu zosakondweretsa Mulungu (Aroma 3:23).

(b) Chifukwa cha machimo athu, tikuyenera kulangidwa ndi kusiyana kwamuyaya ndi Mulungu (Aroma 6:23).

(c) Yesu anafa pamtanda kulipira chilango cha machimo athu (Aroma 5:8; 2 Akorinto 5:21). Yesu anafa m’malo mwathu, kutenga chilango chimene chimayenera ife. Kuuka kwake kumatsimikiza kuti imfa ya Yesu inali yokwanira kulipira machimo athu.

(d) Mulungu amapereka chikhululuko ndi chipulumutso kwa onse amene ayika chikhulupiliro chawo mwa Yesu – kukhulupilira imfa yake ngati malipiro a machimo athu (Yohane 3:16; Aroma 5:1; Aroma 8:1).

Umenewo ndiye uthenga wa chipulumutso! Ngati mwaika chikhulupiliro chanu mwa Yesu Khristu ngati Mpulumutsi wanu, mwapulumutsidwa! Machimo anu onse akhululukidwa, ndipo Mulungu walonjeza kuti sadzakuchokerani kapena kukusiyani nokha (Aroma 8:38-39; Mateyu 28:20). Kumbukirani, chipulumutso chanu chili chotetezedwa mwa Yesu Khristu (Yohane 10:28-29). Ngati mukukhulupilira mwa Yesu yekha ngati Mpulumutsi wanu, mukhonza kukhala ndi chikhulupiliro kuti mudzakhala muyaya ndi Mulungu kumwamba!

2. Pezani mpingo wabwino umene umaphunzitsa Baibulo

Osaganiza za mpingo ngati nyumba yomangidwa. Mpingo ndi anthu. Ndizofunikira kwambiri kuti okhulupilira Yesu Khristu azipemphera wina ndi mnzake. Imeneyi ndiye imodzi mwa zolinga za mpingo. Pakuti tsopano mwayika chikhulupiliro chanu mwa Yesu Khristu, tikukulimbikitsani kwambiri kupeza mpingo wokhulupilira Baibulo m’dera lanu ndikulankhula ndi Abusa. Mudziwitseni za chikhulupiliro chanu chatsopano mwa Yesu Khristu.

Cholinga chachiwiri cha mpingo ndikuphunzitsa Baibulo. Mukhonza kuphunzira m’mene mungayikire malangizo a Mulungu kumoyo wanu. Kudziwa Baibulo ndi kiyi wokhalira ku moyo wa chikhristu chabwino ndi champhamvu. 2 Timoteyo 3:16-17 akuti, “Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu ndipo lipinduritsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero ndi chilangizo cha m’chilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iri yonse yabwino.”

Cholinga chachitatu cha mpingo ndikupembedza. Kupembedza ndikuthokoza Mulungu pa zonse zimene Iye wachita! Mulungu anatipulumutsa. Mulungu amatikonda. Mulungu amatipatsa. Mulungu amatiyang’anira ndikutitsogolera. Sitingamuthokoze chifukwa chiyani? Mulungu ndi wopatulika, wolungama, wachikondi, wachifundo, ndi wodzadza ndi chisomo. Chivumbulutso 4:11 akuti, “Muli woyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemelero ndi ulemu ndi mphamvu, chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, monga m’mene zinalengedwera.

3. Sungani nthawi yolingalira Mulungu tsiku liri lonse.

It is very important for us to spend time each day focusing on God. Some people call this a “quiet time.” Others call it “devotions,” because it is a time when we devote ourselves to God. Some prefer to set aside time in the mornings, while others prefer the evenings. It does not matter what you call this time or when you do it. What matters is that you regularly spend time with God. What events make up our time with God?

Ndizofunika kwambiri kwa ife kupeza nthawi tsiku ndi tsiku kulingalira Mulungu. Anthu ena amayitchula “nthawi yopanda phokoso.” Ena amati “nthawi yolambira,” chifukwa ndi nthawi imene timadzipereka kwa Mulungu. Ena amakonda kusunga nthawi imeneyi m’mawa, pomwe ena amakonda madzulo. Zilibe kanthu kuti mumayitchula mthawi imeneyi chiyani kapena mumasunga nthawi imeneyi nthawi zanji. Chofunikira ndichakuti mumalumikizana ndi Mulungu pafupipafupi. Ndi zochitika ziti zimene zimatipatsa nthawi yolumikizana ndi Mulungu?

(a) Pemphero. Pemphero limangokhala kuyankhula ndi Mulungu. Yankhulani ndi Mulungu zokhudzana ndi inu komanso mabvuto anu. Pemphani Mulungu akupatseni nzeru ndi chisamaliro. Pemphani Mulungu akupatseni zofuna zanu. Muuzeni Mulungu m’mene mumamukondera ndimomwe mumakhutitsidwira ndi zonse zimene amakuchitirani. Limenelo ndiye pemphero.

(b) Kuwerenga Baibulo. Kuwonjezera pa kuphunzitsidwa Baibulo mutchalitchi, sukulu ya lamulungu, ndi/kapena maphunziro a Baibulo – mukuyenera kuwerenga Baibulo pa inu nokha. Baibulo liri ndi chili chonse chimene mungafune kudziwa ndi cholinga chokhala ndi moyo wopambana wachikhristu. Limakhala ndi chisamaliro cha Mulungu cha m’mene mungapangire mfundo zabwino, m’mene mungadziwire zofuna za Mulungu, m’mene mungafalitsire uthenga wabwino kwa ena, ndi m’mene mungakulire muuzimu. Baibulo ndilo Mau a Mulungu kwa ife. Baibulo ndi buku lofunikira limene liri ndi malangizo a Mulungu oyenera kutsatidwa a m’mene tingakhalire moyo wathu momukondweretsa Iye ndikuti ife tikhutitsidwe.

4. Pangani maubale ndi anthu amene angakuthandizeni muuzimu.

1 Akorinto 15:33 akutiuza kuti, “Musanyengedwe: ‘Mayanjano oipa amayipitsa makhalidwe abwino.” Baibulo limatiuza motsindika za momwe anthu “oipa” angatinyengelere. Kukhala ndi anthu amene amachita zinthu zoipa zingatipangitse kukhala ndi chilakolako chopanga nawo zinthuzo. Tikhonza kutengera khalidwe la anthu amene takhala nawo pamodzi. Ndi chifukwa chake ndikoyenera kukhala ndi anthu amene amakonda Mulungu ndikumutsatira Iye.

Yeserani kupeza mzanu kapena awiri, mwina kuchokera kumpingo kwanu, amene angakuthandizeni ndikukulimbikitsani (Aheberi 3:13; 10:24). Uzani amzanu kukudziwitsani mu nthawi imene mukupuma, mukuchita zina zake, ndi mu ulendo wanu ndi Mulungu. Afunseni ngati mungachite chimodzimodzi kwa iwo. Izi sizikutanthauza kuti musiye kucheza ndi amzanu amene sakumudziwa Yesu ngati Mpulumutsi wawo. Pitilizani kukhala mzawo ndipo akondeni. Chabe mungowadziwitsa kuti Yesu anasintha moyo wanu ndipo simungapange zinthu zonse zimene mwakhala mukupanga musanamulandire Yesu mu mtima mwanu. Pemphani Mulungu kuti akupatseni mwayi wogawana Yesu ndi amzanu.

5. Batizidwani.

Anthu ambiri samamvetsetsa za ubatizo. Mau akuti “batiza” amatanthauza kuviika m’madzi. Ubatizo ndi njira ya m’Baibulo yonena poyera za kutembenuka mtima kwako mwa Khristu ndi kudzipereka kwako pakumutsatira Iye. Kuviikidwa m’madzi kumatanthauza kukwiliridwa ndi Yesu. Kuchoka m’madzi kumatanthauza kuuka kwa Khristu. Kubatizidwa ndikudzipereka ku imfa, kuikidwa, ndi kuukanso kwa Yesu (Aroma 6:3-4).

Ubatizo siumene ungakupulumutseni. Ubatizo ndikungolowa m’gawo lomvera, kunena poyera za chikhulupiliro chanu mwa Khristu yekha kuti mukapulumuke. Ubatizo ndi wofunika chifukwa ndi njira yolowera mukumvera – nenani poyera chikhulupiliro chanu mwa Khristu ndikudzipereka kwanu kwa Iye. Ngati muli okonzeka kubatizidwa, muyankhule ndi Abusa.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Ndangoyika chikhulupiliro changa mwa Yesu… Tsopano?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries