settings icon
share icon
Funso

Zikutanthauza chiyani kuvomera Yesu ngati Mpulumutsi wa umoyo wako?

Yankho


Kodi mwalora Yesu Khristu kukhala Mpulumutsi wa moyo wanu? Kuti mumvetse bwino funso limeneli, muyambe mwamvetsetsa mawu akuti “Yesu Khristu,” “umoyo wa munthu,” ndi “Mpulumutsi.”

Kodi Yesu Khristu ndi ndani? Anthu ambiri akhonza kuvomereza Yesu Khristu ndi munthu wabwino, mphunzitsi wabwino, kapenanso m’neneri wa Mulungu. Zinthu izi ndithu ndizoona za Yesu, koma sizikunena zonse za Iye. Baibulo limatiuza kuti Yesu ndi Mulungu muthupi, Mulungu mchifanizo cha munthu (onani Yohane 1:1,14). Mulungu anabwera ku dziko lapansi kudzatiphunzitsa, kutichiritsa, kutikonza, kutikhululukira – ndikutifera! Yesu Khristu ndi Mulungu, Namalenga, Ambuye wopambana. Mwamulandira Yesu ameneyu?

Kodi MPulumutsi ndi chiyani, ndipo ndichifukwa ninji timafuna Mpulumutsi? Baibulo limatiuza kuti tonse tinachimwapo; tonse tinachitapo cholakwika (Aroma 3:10-18). Zotsatira zake za tchimo lathu, tikuyenera kulandira m’kwiyo wa Mulungu ndi chigamulo chake. Chilango chokhacho chakuchimwira Mulungu wamuyaya ndi chilango chamuyaya (Aroma 6:23; Chivumbulutso 20:11-15). Ndichifukwa chake tikufuna Mpulumutsi!

Yesu Khristu anabwera padziko lapansi ndikufa m’malo mwathu. Imfa ya Yesu inali malipiro amuyaya a machimo athu (2 Akorinto 5:21). Yesu anatifera ife chifukwa cha machimo athu (Aroma 5:8). Yesu analipira kuti ife tisatero. Kuuka kwa Yesu kwa akufa kukutitsimikizira ife kuti imfa yake inali yoyenera kulipilira chilango cha machimo athu. Ndichifukwa chake Yesu yekha ndiamene ali Mpulumutsi (Yohane 14:6; Machitidwe a Atumwi 4:12)! Kodi mukukhulupilira mwa Yesu ngati Mpulumutsi wanu?

Kodi Yesu ndi Mpulumutsi wa “umoyo” wanu? Anthu ambiri amaona ngati kupita ku tchalitchi, kuchita miyambo ya zikhulupiliro, ndi/kapena osachita machimo ena ndiye chikhristu. Chimenecho sichikhristu. Chikhristu chenicheni ndi ubale wa umoyo wako ndi Yesu Khristu.kuvomera Yesu kukhala Mpulumutsi wa umoyo wako kukutanthauza kuyika chikhulupiliro cha umoyo wanu mwa Iye. Palibe angapulumuke ndi chikhulupiliro cha ena. Palibe okhululukidwa pakuchita zinthu zina. Njira yokhayo yopulumukira ndikuvomera ndi umoyo wanu Yesu Khristu kukhala Mpulumutsi wanu, kukhulupilira imfa yake ngati malipiro a machimo anu ndi kuuka kwake ngati chitsimikizo cha moyo wanu osatha (Yohane 3:16). Kodi Yesu ndi Mpulumutsi wa umoyo wanu?

Ngati mukufuna kulandira Yesu Khristu kukhala Mpulumutsi wa umoyo wanu, nenani mawu awa kwa Mulungu. Kumbukirani, kunena pemphero ili kapena pemphero liri lonse sikungakupulumutseni. Ndikukhulupilira kokha mwa Yesu ndi zintchito zake zimene anazigwira ndikuzimaliza kumene kungakupulumutseni ku machimo. Pemphero ili ndilongosonyeza kwa Mulungu chikhulupiliro chanu mwa Iye ndikumuthokoza pakukupatsani za chipulumutso chanu. “Mulungu, ndikuzindikira kuti ndakulakwirani ndipo ndili oyenera chilango. Koma ndikhulupilira Yesu Khristu anachitenga chilango chimene chinali choyenera ine kotero kuti mwa chikhulupiliro mwa Iye ndikhonza kukhululukiridwa. Ndikulandira kukhululuka kwanu ndikuyika chikhulupiliro changa mwa inu kuti ndikapulumuke. Ndikulandira Yesu ngati Mpulumutsi wa umoyo wanga! Zikomo chifukwa cha chisomo chanu chodabwitsa ndi kukhululuka kwanu – mphatso ya moyo wosatha! Amen!”

Kodi mwapanga ganizo la Khristu chifukwa cha zimene mwawerenga pano? Ngati ndi choncho, chonde sindikizani batani la “Ndavomera kulandira Khristu lero” pansipa.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Zikutanthauza chiyani kuvomera Yesu ngati Mpulumutsi wa umoyo wako?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries