settings icon
share icon
Funso

Kodi Njira ya Aroma yopita ku cipulumutso ndi ciani?

Yankho


Njira ya Aroma yopita ku cipulumutso ndi njira imodzi imene imagwiritsa nchito mau opezeka m’buku la Aroma kunena za cipulumutso. Ndi njira yapafupi kwambiri yomasulira kufunikira kwake kwa cipulumutso, m’mene Mulungu anakonzera cipulumutso cimeneci, m’mene tingacilandilire, komanso zotulukamo zace mu cipulumutso.

Vesi loyamba ya Njira ya Aroma yopita ku cipulumutso iri pa Aroma 3:23, “Pakuti onse anacimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu.” Ife tonse tacimwa. Tacita zinthu zambiri zosakondweretsa Mulungu wathu. Palibe ngakhale m’modzi wolungama pakati pathu ai. Aroma 3:10-18 apereka cithunzi cozama ca m’mene ucimo umaonekera ukakhala mu miyoyo wathu. Ndipo Mau ena aciwiri pa nkhaniyi, ali pa Aroma 6:23, atiphunzitsa ife tonse za kuipa kwa ucimo – “Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” Cilango cimene ife talandira cifukwa ca macimo athu ndi imfa. Si imfa ya thupi cabe ai, komanso imfa ya muyaya ya mzimu.

Vesi lacitatu ya Njira ya Aroma yopita ku cipulumutsoiri pa Aroma 6:23, “Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” Aroma 5:8 akuti, “Koma Mulungu atsimikiza kwa ife cikondi cace ca mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife cikhalire ocimwa, Kristu adatifera ife.” Yesu anatifera ife! Imfa yace ya Yesu inalipira mlandu wa macimo athu. Ndipo kuuka kwa Yesu kuonetsa kuti Mulungu analandira imfa yace kukhala dipo la macimo athu.

Cacinai copezeka mu Njira ya Aroma yopita ku cipulumutsociri pa Aroma 10:9 “pakuti ngati udzabvomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.” Cifukwa ca imfa ya Yesu m’malo mwathu, ife cimene tiyenera kucita cabe ndi ku khulupirira mwa Iye ndi kudalira kuti imfa yace inaticotsera cilango ca macimo athu – motero tipulumutsidwa! Pa Aroma 10:13 mau akuti, “pakuti, amene ali yense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.” Yesu anafa kulipira cilango ca macimo athu ndipo motero Iye atiombola ife kucionongeko cosatha. Cipulumutso, kukhululukiridwa kwa macimo, kulipo kwa iwo onse okhulupirira mwa Yesu kukhala Ambuye ndi Mpulumutso wao.

Gawo lotsiriza la Njira ya Aroma yopita ku cipulumutso inena pa zotulukamo mu cipulumutso. Pa Aroma 5:1 pali mau awa, “Popeza tsono tayesedwa olungama ndi cikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu.” Mwa Yesu Kristu titha kukhala ndi ubale wabwino ndi Mulungu. Aroma 8:1 atiphunzitsa, “Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa. Pakuti cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo la ucimo ndi la imfa.” Cifukwa ca imfa ya Yesu m’malo mwathu sitidzatsutsidwa cifukwa ca macimo athua. Ndipo potsiriza tili ndi lonjezano ili lokoma locokera kwa Mulungu lopezeka pa Aroma 8:38-39 “Pakuti ndatsimikiza mtima kuti imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera m’tsogolo, mphamvu, msinkhu, kuzama, kapena cholengedwa china ciliconse, sicidzatha kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu cimene cili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.”

Kodi mungakonde kutsatira Njira ya Aroma yopita ku cipulumutso? Ngati nditero, mutha kupemphera pemphero ili kwa Mulungu. Kupemphera pemphera limeneli ndi njira imodzi yakutsimikiza kwa Mulungu kuti cipulumutso canu citheka cabe ndi Yesu Kristu. Mau okha a pemphero satha kukupulumutsani koma cikhulupiriro mwa Yesu Kristu ndico cimene cipulumutsa. “Mulungu ndidziwa ndakucimwirani ndipo ndiyenera kulangidwa kuopsya. Koma Yesu analandira cilango canga kuti mwakukhulupirira Iye, ine ndikhululukiridwe. Mundithandize kuika cikhulupiriro canga mwa Inu kuti ndilandire cipulumutso. Zikomo cifukwa ca cisomo canu cakuya ndi cikhululukiro canu – cimene ndi mphatso ya moyo wosatha! Amen!”

Kodi mwapanga ganizo la Khristu chifukwa cha zimene mwawerenga pano? Ngati ndi choncho, chonde sindikizani batani la “Ndavomera kulandira Khristu lero” pansipa.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi Njira ya Aroma yopita ku cipulumutso ndi ciani?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries