settings icon
share icon
Funso

Kodi Yesu Khristu ndiye yani?

Yankho


Mosiyana ndi funso “Kodi Mulungu alipo?” anthu ochepa amafunsa ngati yesu Yesu Khristu analipo. Mwachidziwikire ndizovomereka kuti Yesu analidi munthu amene anakhalapo pa dziko lapansi ku Isiraeli zaka 2000 zapitazo. Msutso umayamba nkhani za umunthu wa Yesu zikayamba kukambidwa. Pafupifupi mipingo ikuluikulu yambiri imaphunzitsa kuti Yesu anali Mneneri kapena Mphunzitsi wabwino kapena munthu wa Mulungu. Vuto ndilakuti Baibulo limatiuza kuti Yesu anali oposa Mneneri, Mphunzitsi wabwino, kapena munthu wa Mulungu ku nthawi zonse.

C.S. Lewis m’buku lake Mere Christianity analemba motere: “Ndikuletsa aliyense kunena zopusa zomwe anthu amakamba zokhudza Iye (Yesu Khristu): Ndili wokonzeka kulandira Yesu ngati Mphunzitsi wamkulu wa makhalidwe abwino, koma sindikuvomereza zoti Iye ndi Mulungu.” Ichi ndi chinthu chimodzi choti tisamanene. Munthu yemwe anali munthu chabe ndipo ndikuyankhula zinthu zosiyana ndi zomwe Yesu anayankhula sadzakhala mphunzitsi wa khalidwe labwino koma adzakhala osokonekera – chimodzimodzi ndi munthu amene ananena kuti iye ndi dzira losakidwa – apo ayi adzakhala satana wakumoto. Pangani chisankho chanu. Munthu ameneyu anali,nipo ali, mwana wa Mulungu, kapena ndi wamisala kapenanso wopanda pake. Mukhunza kumutenga ngati wopusa, mukhonza kumulavulira ndi kumupha ngati satana; kapena mukhonza kumugwadira pamapazi ake ndikumutcha Ambuye komanso Mulungu. Koma tiyeni tisapange maganizo osokonekera okhudzana ndi Iye kukhala Mphunzitsi wabwino wa munthu. Mwayi umenewo sanawupereke kwa ife. Sanafune kutero.”

Ndiye, kodi Yesu amati Iye ndi yani? Nanga Baibulo likuti Iye ndi yani? Poyamba, tiyeni tiwone mawu a Yesu pa Yohane 10:30, “Ine ndi Atate ndife amodzi.” Kuona koyamba, izi zikhonza kuoneka ngati sizikunena kuti Iye ndi Mulungu. Komabe, onani m’mene Ayuda anachitira ku mawu ake, ‘“Pantchito yabwino sitikuponyani miyala,’ anayankha motero Ayuda, ‘koma chifukwa cha mwano, ndikuti inu muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu’” (Yohane 10:33). Ayuda anamva mawu a Yesu ngati kunena kuti Iye ndi Mulungu. Mu ndime zotsatirazi, Yesu sanawakonze Ayuda ponena kuti, “Ine sindinanene kuti ndine Mulungu.” Uku ndikusonyeza kuti Yesu amanenadi kuti Iye ndi Mulungu ponena kuti, “Ine ndi atate ndife amodzi” (Yohane 10:30). Yohane 8:58 ndi chitsanzo china: ‘“Indetu, indetu ndinena kwa inu,’ Yesu anayankha, ‘asanayambe kukhala Abrahamu, ndipo ine ndilipo!’” mobwerenza, mukuyankha kwake, Ayuda anatola miyala kuti amponye Yesu (Yohane 8:59). Yesu podzinena kuti “Ine ndine” kunali kudzitchula kwa dzina la Mulungu laku Chipangano Chakale (Eksodo 3:14). Ndichifukwa chiyani Ayuda anafunanso kumuponya miyala Yesu ngati sananene zinthu zimene amazikhulupilira kuti ndi mwano, monga, kudzinena kuti ndi Mulungu.

Yohane 1:1 akuti “Mawu anali Mulungu.” Yohane 1:14 akuti “Mawu anasanduka thupi.” Izi zikusonyeza poyera kuti Yesu ndi Mulungu mu thupi. Thomasi ophunzira wake wa Yesu ananena kwa Yesu, “ambuye wanga ndi Mulungu wanga” (Yohane 20:28). Yesu sanamukonze iye. Mtumwi Paulo anamutcha Iye ngati, “…Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu” (Tito 2:13). Mtumwi Petro ananena chimodzimodzi, “…Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu” (2 Petro 1:1). Mulungu Atate ndiyenso mboni ya amene ali Yesu, “Koma za Mwana amene amanena, ‘Mpando wanu wa chifumu, Mulungu, udzakhala ku nthawi zosatha, ndipo chilungamo chidzakhala ndodo ya chifumu mu ulemelero wanu.” Alosi a Yesu ku Chipangano Chakale amamutcha Iye kuti, “Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa, ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake. Mdipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa Wauphungu, Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa Mtendere.” (Yesaya 9:6).

Kotero, monga C.S. Lewis ananenera, sikusankha kukhulupilira kuti Yesu anangokhala Mphunzitsi wabwino. Yesu ananena poyera ndipo sanakane kuti Iye anali Mulungu. Ngati Iye si Mulungu, ndiye kuti Iye ndi wabodza, kotero si Mlosi, Mphunzitsi wabwino, kapena munthu wa Mulungu. Pofunafuna kulongosola bwinobwino mawu a Yesu, “wophunzira” amakono amanena “Yesu weniweni wa mbiri yakale” sananene zambiri mwa zinthu zimene Baibulo limanena za Iye. Ife ndiyani kuti titsutse mawu a Mulungu okhudzana ndi zimene Yesu ananena kapena sananene? Ndizotheka bwanji kuti “wophunzira” zaka mazana awiri kuchotsedwa kwa Yesu kukhala wozindikira kwambiri mu zimene Yesu ananena kapena sananene kuposa amene anakhala naye, kutumikira naye, ndipo anaphunzitsidwa ndi Yesu Amene (Yohane 14:26).

Ndi chifukwa chiyani funso loti Yesu ndiyani liri lofunikira? Ndichifukwa chiyani kuli kofunika kudziwa ngati yesu ali Mulungu kapena ayi? Chifukwa chofunikira kwambiri chimene Yesu akuyenera kukhalira Mulungu ndichakuti ngati Iye asali Mulungu, imfa yake siikanakhala yoyenera kulipilira chilango cha machimo a dziko lonse lapansi (1 Yohane 2:2). Ndi Mulungu yekha angalipire chilango chopanda mathero ngati chimenechi (Aroma 5:8; 2 Akorinto 5:21). Yesu akuyenera kukhala Mulungu kuti athe kulipira ngongole yathu. Yesu akuyenera kukhala munthu kuti afe. Chipulumutso chilipo pokhapokha ukakhulupilira mwa Yesu Khristu. Yesu kukhala M’modzi mwa Milungu ndi chifukwa ali njira yokhayo yakuchipulumutso. Yesu kukhala m’modzi mwa Milungu ndi chifukwa Iye ananena , “Ine ndine njira ndi choonadi ndi moyo. Palibe adza kwa Atate koma kudzera mwa ine” (Yohane 14:6).

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi Yesu Khristu ndiye yani?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries