settings icon
share icon
Funso

Kodi munthu akafa, akhalanso ndi moyo?

Yankho


Kodi pali moyo munthu akafa? Baibulo linena kuti, “Munthu wobadwa ndi mkazi Ngwa masiku owerengeka, nakhuta mabvuto, Aturuka ngati duwa, nafota; Athawa ngati mthunzi, osakhalitsa…Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi” (Yobu 14:1-2, 14)?

Monga Yobu, if tonse mwina taganizirapo pa funso limeneli. Kodi cimene cimacitika kwenikweni tikafa ndi ciani? Kodi timakutha kukhalako? Kodi aliyense munthu amapita kumalo amodzi, kapena timapita kumalo osiyanasiyana? Kodi ndizoonadi kuti kuli kumwamba ndi gehena kapena izizi ziri cabe m’maganizo ya anthu?

Baibulo linena momveka bwino kuti si moyo cabe uliko kutsogolo kwa imfa koma kuli moyo wosatha wokhala ndi ulemerero kwambiri, “koma monga kulembedwa, Zimene diso silinaziona, ndi khutu silinazimva, Nisizinalowa mu mtima wa munthu, Zimene ziri zonse Mulungi anakonzereratu iwo aku mkonda iye” (1 Akorinto 2:9). Yesu Kristu, Mulungu m’thupi, anadza ku dziko lapansi kudzatipatsa mphatso ya moyo wosatha. “Koma Iye analasidwa cifukwa ca zolakwa zathu, natundudzidwa cifukwa ca mphulupulu zathu; cilango cotitengera ife mtendere cinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yace ife taciritsidwa” (Yesaya 53:5).

Yesu ananyamula cilango ca aliyense munthu kapena aliyense wa ife cimene tikadayenera kulangidwa ndipo Iye anapereka moyo wace m’malo mwathu. Patapita masiku atatu, Iye anaonetsa kupambana kwace pogonjetsa imfa pouka m’manda, m’mzimu ndi m’thupi. Iye anakhala ndithu pa dziko lapansi kwa masiku makumi anai (40) ndipo anaonekera kwa anthu ambirimbiri amene anacitira umboni za kuuka kwace, Iye asanapite kumwamba kwa Atate. Aroma 4:25 akuti, “amene anaperekedwa cifukwa ca zolakwazathu, naukitsidwa cifukwa ca kutiyesa ife olungama.”

Kuuka kwa Kristu ndi cinthu colembedwa bwino kwambiri. Paulo mtumwi anauza Akristu kuti ngati afuna afunse iwo amene anamuona Iye ngati zimenezo ndi zoonadi. Ndipo palibe amene anatsutsana naye Paulo pa coonadi ici. Kuukwa ca Kristu ndipo pagona cikhulupiriro ca Cikristu; cifukwa Kristu anaukitsidwa kwa akufa, tikhala ndi cikhulupiriro ifenso kuti tikafa tidzaukitsidwa.

Paulo anacenjeza Akristu ena woyamba amene sanakhulupirire ndipo anati, “Koma ngati Kristu alalikidwa kuti waukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanji kuti kulibe kuuka kwa akufa? Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, Kristunso sanaukitsidwa” (1 Akorinto 15:12-13).

Kristu anali woyamba pakati pa iwo oukitsidwa kukhalanso ndi moyo ndipo ciukitso cake cinali cakupereka moyo kwa anthu onse. Imfa ya thupi inadza kupyolera mwa munthu m’modzi, Adamu, kumene ife tonse ticokerako. Komai wo onse amene alandiridwa mu banja la Mulungu mwa kukhala ndi cikhulupiriro mwa Yesu Kristu apatsidwa moyo watsopano (1 Akorinto 15:20-22). Monga momwe Mulungu anaukitsira thupi la Yesu, moteronso matupi athu adzaukitsidwa pakufikanso kwa Yesu (1 Akorinto 6:14).

Ngakhale kuti potsiriza pace tonsefe tidzaukitsidwa, si aliyense amene adzapita kumwamba kukakhala ndi Mulungu. Coyamba, cisankho ciyenera kucitika ndi munthu wina aliyense mu moyo wace kuti adziwe bwino kumene iye adzakhala pakutha kwa ciweruzo. Baibulo linena kuti, kwaikidwa kuti munthu adzafa kamodzi ndipo pambuyo pace kudzakhala ciweruzo (Ahebri 9:27). Iwo amena anatsukidwa ndi kuyeretsedwa adzapita ku moyo wosatha kumwamba kwa Atate, ndipo iwo wosakhulupirira adzatumizidwa kucilango cosatha, kapena ku gehena (Mateyu 25:46).

Gehena, monga kumwamba, si malo oyerekezerako malo ena apansi pano ai, koma ndi malo oonadi. Ndi malo kumene onse oipa, wosakhulupira Yesu Kristu adzakhala mu moyo wao wonse, pakutha kwa ciweruzo ndipo kumalo amenewo adzakumana ndi mkwiyo wa Mulungu. Iwo adzavutika, adzalira, ndipo adzacita manyazi, adzamva cisoni ndipo adzasowekeratu ulemu.

Gehena, amati ndi malo oonga dzenje koma lopanda mathero ake (Luka 8:31; Chibvumbulutso 9:1), ndi Nyanja ya moto, woyaka ndi safure kumene onse okhalako adzazunzika usana ndi usiku mosalekeza ku nthawi zonse (Chibvumbulutso 20:10). Ku gehena kudzakhala kulira ndi kukukuta mano kuonetsa kuti pamenepo zinthu zaipadi kwambiri komanso adzaonetsa ukali (Mateyu 13:42). Ndi malo kumene mphutsi sizikufa ai ndipo moto siuzima (Marko 9:48). Mulungu sakondwera ndi imfa ya munthu wocimwa kapena woipa ndipo afunitsitsa iwo kuti atembenuke kuleka njira zoipa ndi kukhala ndi moyo (Ezekieli 33:11). Koma Iye sadzakakamiza wina aliyense kumutsata Iye; tikasankha kumukana Iye, kulibe m’mene zinthu zitha kukhalira koma adzatipatsa cimene tifuna – kukhala patali ndi Iye.

Moyo wa padziko ulingati umoyo wokonzekera mayeso amene adzabwera patsogolo. Kwa okhulupirira kutero ndi kukhala ndi moyo wosatha pamaso pa Mulungu. Kodi tilungamitsidwa bwanji komanso tilandira bwanji moyo wosatha? Pali cabe njira imodzi yokha – mwa cikhulupiro ndi kukhulupirira mwa Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu. Yesu anati, “Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo; wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ici?” (Yohane 11:25-26).

Mphatso ya ulere ya moyo wosatha ilipo kwa onse, koma ifuna kuti ifeyo tizikane tokha ku zokondweretsa za dziko ndi kuzipereka kwa Mulungu ngati nsembe. “Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye” (Yohane 3:36). Sitidzapatsidwa m’pata wakulapa macimo athu tikafa cifukwa tikaonana ndi Mulungu wathu maso di maso, tidzakhala opanda cisankho koma kukhulupirira mwa Iye yekha. Mulungu afuna ife kuti tibwere kwa Iye mwa cikhulupiro ndi cikondi pamene tili ndi moyo. Tikabvomereza imfa ya Yesu Kristu kukhala malipiro mulandu wathu wa macimo pamaso Mulungu, adzatipamoyo wabwino padziko lapansi komanso moyo wosatha mwa Yesu Kristu wa kunthawi zonse.

Ngati mufuna kulandira Yesu kukhala Mpulumutsi wanu, pali pemphero losavuta pano. Kumbukirani kuti pemphero ili, kapena pemphero lina lirilonse silidzakupulumutsani ai. Ndikukhulupirira mwa Yesu yekha cabe kumene kumabweretsa cipulumutso. Pemphero ili ndi njira ina cabe yofunikira m’mene tionetsera cikhulupiriro kwa Mulungu ndi kumuyamika cifukwa ca cipulumutso. “Mulungu ndidziwa kuti ndakucimwirani ndipo ndiyenera kulangidwa cifukwa ca macimo anga. Koma Yesu Kristu anatenga cilango canga cimene ndikadalangidwa naco, kuti mwa kukhala ndi cikhulupiro mwa Iye ndikhululukiridwa zoipa zanga zonse. Ndiika cikhulupiriro canga conse mwa Iye kuti ndidzapulumutsidwa. Zikoma cifukwa ca njira yanu yokoma ya cipulumutso, cisomo ndi cikhululukiro – zimene ziri mphatso ya moyo wosatha! Amen!”

Kodi mwapanga ganizo la Khristu chifukwa cha zimene mwawerenga pano? Ngati ndi choncho, chonde sindikizani batani la “Ndavomera kulandira Khristu lero” pansipa.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi munthu akafa, akhalanso ndi moyo?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries