settings icon
share icon
Funso

Kodi Baibulo ndilo Mau a Mulungu zoonadi?

Yankho


Yankho lathu pa funso limeneli lidzatilangiza m’mene ife timverera Baibulo ndi kufunikira kwace pa umoyo wathu, kuphatikiza magawo onse a umoyo. Ngati Baibulo zoonadi ndi Mau a Mulungu, ndiko kuti tiyenera kukondwera ndi kuyamikira, tiyenera kulisanthula, tiyenera kumvera mauwo, ndi kukhulupirira kopanda kukaikira konse. Baibulo ndi Mau a Mulungu, ndiko kulikana ndiko kukananso Mulungu mwini.

Kuona pa cifukwa kuti Mulungu watipatsa Baibulo, pamenepo tionapo cikondi cake pa ife. Mau akuti “chibvumbulutso” angotanthauza kuti Mulungu analumikizana ndi anthu kuwadziwitsa m’mene Iye aliri, ndi cimene Iye ali komanso kutidziwitsa m’mene tingakhalire ndi ubale wabwino ndi Iye. Kuti Mulungu sanalole kuti zinthu izi zauzimu tizione, sakadalo kuzibvumbulutsa kwa ife anthu mu Baibulo.Ngakhale kuti mu Baibuli chibvumbulutso ca iye mwini Mulungu cinapatsikwa kwa nthawi yaitali monga zaka 1,500, koma chibvumbulutsoco ciri ndi zonse zimene ziri zofunikira kuti munthu adziwe Mulungu ndi kukhala ndi ubale wabwino ndi Iye. Ngati baibulo ndi Mau a Mulungu zoonadi, ndiko kuti ndiyo iri ndi mphamvu yonse pa zonse za cikhulupiriro, za cipembedzo, ndi za cikhalidwe.

Funso limene ife tiyenera kuzifunsa ndi lakuti, Baibulo ndilo Mau a Mulungu losiyana ndi mabuku ena abwino? Kodi Baibulo lisiyana bwanji ndi mabuku ena onse a zauzimu amene analembedwa kumbuyuku? Kodi pali umboni wotani kuti Baibulo ndilo Mau a Mulungu oonadi? Mafunso otere kapena amenewa ayenera kulowapo mwakuya ndithu kuti tikhale naco citsimikizo ceniceni ndi cokwanira bwino ca zomwe Baibulo limanene kuti limenelo ndiye Mau a Mulungu, kuti popeza kunalembedwa kuti, Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu polembedwa ndi kuti ndiyokwanira ndi lofikapo pa zonse zokhuza cikhulupiriro ndi cipembedzo.

Palibenso kukaikira kuti Baibulo linena kuti ndilo Mau a Mulungu eni eni. Izi zionekera m’mau amene Paulo analembera kwa Timoteo: “…ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira cipulumutso, mwa cikhulupiriro ca mwa Kristu Yesu. Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa ciphunzitso, citsutsano, cikonzero, cilangizo ca m'cilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kucita nchito iri yonse yabwino” (2 Timoteo 3:15-17).

Pali maumboni okwanira bwino opezeka mkati ndi kubwalo kuti Baibulo ndi Mau a Mulungu oonadi. Umboni wamkati ndi zinthu zimene Baibulo linena za gwero lace la uzimu. Umboni wina woonekeratu kuti Baibulo ndi Mau a mulungu oonadi upezeka m’kugwirizana kwake kwa magawo ndui mau ace. Ngakhale kuti iri ndi mabuku okwanira makhumi asanu ndi limodzi kudza mphambu zisanu ndi limodzi (66) olembedwa kucokera ku makontinenti (dziko lalikuru lokhala ndi maiko ena mkati mwace, mwacitsanzo Afrika) atatu, mu zilankhulo zosiyanasiyana pakati pa zaka zakurengedwa ngati 1,500 ndipo olemba ndi osacepekera pa anthu makhumi anai (40) amene ankagwira nchito zao zosiyanasiyana, ndipo ngakhale nditero Mau ace a mu Baibulo ndi wogwirizana bwino kopanda kutayana konse. Umodzi umenewu wa buku limeneli ndiwodabwitsa kwambiri ndipo usiyana ndi mabuku ena onse ndipo zimenezo zionetsadi kuti Baibulo liri ndi gwero lenileni la umulungu pa Mau amene Mulungu analembetsa osankhidwa ace.

Cina cotsimikiza za uboni wotsimikiza kuti Baibulo ndi Mau a Mulungu oonadi, ndi mau ace acinenero opezeka mkati mwace. Baibulo liri ndi ma acinenero ambiri mbiri okhuzana ndi tsogolo la maiko paokhapaokha kuikapo dziko la Israyeli, mizinda ina ndi mitundu ina ya anthu. Zinenero zina anena za kubwera kwa Iye wokhala Mesiya, Mpulumutsi wa iwo onse amene adzakhulupirira mwa Iye. Kusiyana ndi zinenero zopezeka m’mabuku azipembedzo zina kapena zinenero za anthu monga Nostradamusi, zinenero za mu Baibulo ndi zozama. M’cipangano Cakale muli mau osacepekera pa mazana (300) atatu acinenero onena za Yesu Kristu. Mauwo sananene cabe za malo kumene iye (Yesu) adzabadwira ndi kunena za makolo ace cabe ai, koma ananenanso za momwe Iye adzafera ndi kuukanso kwace. Palibe nzeru kapena ciganizo cokwanira cimene cingathe kumasulira za zinenero zimenezi koposa kugwiritsa nchito za umulungu. Palibe bulu lina la zauzimu kapena za cipembedzo imene ili ndi zinenero zotero zimene zikwaniritsidwa mofikapo munthawi yace.

Cacitatu cotsimikiza za uboni wotsimikiza kuti Baibulo ndi liri ndi gwero la umulungu ndi mphamvu ndi udindo wa mau ace. Koposa mfundo ziwiri zoyambazo ciganizo ici sicitanthauza kuti umboni wa mphamvu ya gwero la umulungu mu Baibulo ndi locepekera ai. Mphamvu ya Baibulo ndiloposa mabuku ena onse olembedwa. Ulamuliro ndi mphamvu ya baibulo umaonekera mwa miyoyo yambirimbiri imene yakhuzidwa ndi kusinthika cifukwa ca mphamvu ya Mau a Mulungu. Anthu ogwiritsa nchito mankhwala ozunguza bongo, aciritsidwa ndi mau ake, anthu okonda mcitidwe wogonana naonso amasulidwa ku nsinga zao, anthu ngakhale iwo woyesedwa ankhanza ndi olimba mtima atembenuzidwa ndi Baibulo, mbala zagonja ndi Mau a Mulungu, ndipo ocimwa adzudzulidwa ndi mauwo, ndipo iwo okhala ndi cizondo naonso ayamba kukonda buku limeneli. Baibulo liri ndi mphamvu yapadera kwambiri imene itheka cabe kugwira nchito cifukwa cakuti mauwo ndi Mau a Mulungu oonadi.

Palinso umboni wina wakubwalo oonetsa kuti Baibulo ndi Mau a Mulungu oonadi. Cina ca ico ndi mbiri yace ya Baibulo. Cifukwa cakuti Baibulo linena za zinthu zocitika mu mbiri zinthu zapezeka kuti ndizoonadi ndipo zinacitika monga mwa Mau. Anchito ya kudziwa za mbiri yakale amene amakumba-kumba m’malo oganiziridwa kuti munali zakuti-zakuti zopezeka zina zakhala monga momwe Baibulo linanenera ndendende. Komanso zolemba zopezeka zokhuzana ndi Baibulo nazonso zipezeka kuti sizisiyana ndi comwe Baibulo linena. Baibulo liri ndi mau a coonadi ngakhale pamene linena pa mbiri ya anthu kapena malo ndipo ena azamaphunziro akuya, acitiradi umboni za ici ndikutsimikiza za coonadi cake, ca Mau a Mulungu.

Palinso umboni wina wakubwalo oonetsa kuti Baibulo ndi Mau a Mulungu ndi ungwiro ndi kusakikitsa kwa olemb. Monga tanenapo kale poyamba, Mulungu anagwiritsa nchito anthu osiyanasiyana komanso anchito zosiyanasiyana kulemba Mau ace. Mwa kucita kafukufuku ka awa anthu, olemba, tipeza kuti iwo anaima pa cilungamo ndi coonadi. Tidziwa ici cifukwa anthu amenewa pakati pa mavuto ndi cipsinjo analola kualandira imfa yoipa cifukwa ca kukhulupirira pa Mau a Mulungu ndi zimene Mulungu anali kuwanong’oneza. Anthu amene analemba Cipangano Catsopano ndi anthu ena ambirimbiri (1 Akorinto 15:6) anadziwa coonadi ca uthenga wao cifukwa iwo anali atakhala ndi Yesu Kristu pa nthawi ya umoyo wao pamene Iye anaukitsidwa kwa akufa, Kuona Yesu atauka, kunabweretsa mphamvu pakucita nchito ndipo cilimbikitso pa kukhulupirira Yesu. Iwo anacoka m’malo m’mene anali kubisala ndi kuzipereka kuti akhoza kufa pofalitsa uthenga wabwinowo. Umoyo wao ndi imfa zao zionetsadi kuti ndizoonadi kuti Baibulo ndi Mau a Mulungu.

Umboni wina wakubwalo oonetsa kuti Baibulo ndi Mau a Mulungu ndiko kusaonongeka kwace. Cifukwa ca kufunikira kwace ndi kuti bukulu ndi Mau a Mulungu, anthu odana ndi Baibulo ayesetsa kucita zothekera zonse kuti alicotse pansi pano bukulo. Ngati pali buku limene anthu ena ambiri ayesetsa kuti aliononge, ndi Baibulo, osati buku lina lirilonse ai. Kuyambira kalekale pa ulamuliro wa mfumu ya Ciroma yodziwika kuti Diocletian, kufikira kuli adzitsogoleri ena ankhanza zao m’maiko ena, kuikapo anthu okana kuti kulibe Mulungu, komanso iwo akusamvetsa za bukulo ayesetsa koma Baibulo lakalabe likukhala ku nthawi zonse. Ndiponso kufikira lero lino ndilo buku limene lasindikizidwa kwambiri koposa mabuku ena ndithu.

Kucokera kalekale, anthu ena okaika, aona baibulo kukhala ngati nkhani yakale imene anthu angakhulupirire, koma anthu oona pa mbiri yakumbuyo komanso ukumba m’malo m’malo kuti adziwe za khalidwe la anthu ndi zakumbuyo, atsimikizira kukhalako kwa zambiri zopezeka mu Baibulo. Otsutsa ena amati Baibulo ndilakalekale motero ndi buku losafunika, koma ziphunzitso zake zambiri za Baibulo zikuthandiza anthu apa dziko kukhala bwino. Otsutsa ndi kudana nalo Baibulo ena ndi anthu a nchito za sayansi, anthu amabunziro oona pa kaganizidwe ka munthu komanso ena ambiri a zandale, koma Baibulo likhalabe lokwanira ndiponso la coonadi monga pa nthawi pamene inalembedwa. Ndi buku limene kwa zaka 2,000 ndi kupyolapo lasintha miyoyo ndi cikhalidwe ca anthu. Ngakhale kuti adani ayesetsa njira zambiri kufuna kuti Baibulu lioneke ngati lopanda nchito koma baibulo likhalabe cikhalire likulankhula ku miyoyo ya anthu ndipo anthu ambiri akusintha cikhalidwe cifukwa ca kulondola zolembedwamo. Ngakhale kuti oyesa kuliononga Baibulo mwa njira zao zambiri ayesetsa, koma alephera ndithu, ndipo zimenezo zionetsa coonadi cake ca Baibulo kuti amenewo ndi Mau a Mulungu amene akhala otetezedwa ndi Iye ku nthawi zonse. Tisadabwe ai kuti ngakhale kuti anthu ena aukile Baibulo zocita zao zilepherabe ndipo Baibulo likhalabe losasinthika kunthawi zonse. Pakuti Yesu anati, “Thambo ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita” (Marko 13:31). Kuona umboni umene ulipo, wina aliyense akhoza kunena mosakaikira konse kuti, Inde, Baibulo ndi Mau a Mulungu.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi Baibulo ndilo Mau a Mulungu zoonadi?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries