Funso
Kodi a Kristu anenapo bwanji pa nkhani za kudzipha wekha? Kodi Baibulo linena ciani pakudzipha wekha?
Yankho
Baibulo linena za anthu asanu ndi m’modzi kapena kuti sikisi (6) amene anadzipha okha Abimeleki (Oweruza 9:54), Saulo (1 Samueli 31:4), wankhondo wa Sauli (1 Samueli 31:4-6), Ahitofeli (2 Samulei 17:23), Zimri (1 Kings 16:18), ndi Yudasi (Mateyu 27:5). Asanu (5) a anthuwa anali oipa (ndipo sitikumva zambiri zonena za wankhondo wa Sauli). Ena aganizira kuti nayenso Samsoni ali pa gawo ya anthuwa odzipha okha (Oweruza 16:26-31), koma colinga ca Samsoni cinali kufuna kupha Afilisiti, osati kudzipha ai. Baibulo iona pa kudzipha kukhala ndithu ngati kupha wina – ndipo munthu akatero amenena kuti wadzipha yekha. Mulungu yekha ndiye amene ali ndi mphamvu ndi ulamuliro pa umoyo wa munthu m’mene munthuyo angafere.
Monga wa Baibulo, kudzipha sindiyo mfungulo yoonetsa kuti munthu akalowa Kumwamba. Munthu woipa akadzipha, palibe cimene iyeyo wacita koposa kufulumiza ulendo wace waku gehena. Munthu ameneyo wodzipha yekha adzakhala ku gehena cifukwa ca kukana cipulumutso codzera mwa Kristu, osati cifukwa cakuti iyeyo anadzipha ai. Kodi Baibulo linena ciani za Mkristu wodzipha yekha. Baibulo liphunzitsa kuti nthawi imene tibvomereza ndi kukhulupirira Yesu, tipatsidwa umoyo wosatha (Yohane 3:16). Monga mwa Baibulo, a Kristu adziwa mopanda cikaiko ciri conse kuti iwo ali ndi umoyo wosatha (1 Yohane 5:13). Palibe cimene cingawalekanitse iwo ndi Mulungu (Aroma 8:38-39) Ngati palibe “cinthu colengedwa” cimene cingawalekanitse iwo ndi cikondi ca Mulungu, ndiko kuti ngakhale Mkristu wodzipha yekha amene akhala “wolengedwa” motero ngakhale imfa yotero siingathe kuwalekanitsa iwo pa cikondi ca Mulungu. Yesu anafera macimo athu onse, ndipo ngati Mkristu weniweni, pa nthawi ya zovuta, zauzimu kapena za thupi, iye adzipha yekha, imeneyo ndi cimo limene mwazi wa Yesu umayeretsa ndithu.
Kudzipha kukhalabe cimo loipa pamaso pa Mulungu. Monga mwa Baibulo, kudzipha wekha ndiko kulakwa; ndi koipa. Ngati munthu amene adziyesa ndi kudziwika kuti ali ndi cikhulupiriro mwa Yesu, wotero akadzipha, pamenepo payenera cikaiko ca umoyo wace wauzimu. Palibe nyengo imene iyenereza Mkristu kutenga moyo wace mwa kudzipha. Akristu mu umoyo wao ayenera kuonetsa Krisstu ndipo imfa ya iwo iri m’dzanja la Mulungu osati la iwo ai. Ngakhale mau awa sanena za kudzipha, 1 Akorinto 3:15 pamenepo pali mau othandiza pa cimene cimacitika Mkristu akadzipha yekha: “koma iye yekha adzapulumutsidwa; koma monga momwe mwa moto.”
English
Kodi a Kristu anenapo bwanji pa nkhani za kudzipha wekha? Kodi Baibulo linena ciani pakudzipha wekha?