Funso
Kodi Cikristu nciani ndipo Akristu amakhulupirira ciani?
Yankho
Pa 1 Akorinto 15:1-4 mau akuti, “Ndipo ndikudziwitsani, abale, Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani inu, umenenso munalandira, umenenso muimamo, umenenso mupulumutsidwa nao ngati muugwiritsa monga momwe ndinalalikira kwa inu; ngati simunakhulupira cabe. Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, cimenenso ndinalandira, kuti Kristu anafera zoipa zathu, monga mwa malembo; ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lacitatu, monga mwa malembo.”
Mwacidule pamenepo ndipo pagona cikhulupiriro ca Ukristu. Cikhulupiro cimeneci cisiyanadi ndi zikhulupiro za zipembedzo zina. Cikristu makamaka caima pa ubale osangokhala pa cipembedzo cokha. M’malo mokhala ndi mndandanda wa zocita ndi zoletsedwa, colinga ca ciKristu ndi kukhala ndi ubale weniweni ndi Mulungu pakuyenda ndi Iye. Ubale uyu utheka cifukwa ca nchito ya Yesu Kristu ndi Mzimu Woyera mu moyo wa Mkristu.
Akristu akhulupirira kuti Lemba liri lonse mu Baibulo “adaliuzira” Mulungu ndi kuti Mau a Mulungu ndi kuti Mau a Mulungu ndi okwanira pa ciphunzitso conse ca ci Kristu (2 Timoteo 3:16; 2 Petro 1:20-21). Akristu akhulupirira mwa Mulungu m’modzi mwa Atatu – Atate, Mwana (Yesu Kristu) ndi Mzimu Woyera.
Akristu akhulupirira kuti munthu analengedwa ndi cilingo coti iyeyo akhale pa ubale ndi Mulungu koma pamene ucimo unalowa m’dziko lapansi unalekanitsa ubalewo (Aroma 3:23; 5:12). Cikristu citiphunzitsa kuti Yesu anakhala ndi kuyenda m’dziko lapansi ngati Mulungu komanso munthu (Afilipi 2:6-11) ndipo anafa pa mtanda. Akristu akhulupirira kuti anafa Yesu, anaikidwa m’manda, Iye anaukitsidwa ndipo tsopano ali pa dzanja la manja la Mulungu Atate, ndipo apempherera onse okhulupirira (Ahebri 7:25). Cikristu cimafalitsa uthenga wa imfa ya Yesu kuti mwa imfa imeneyo mlandu wa macimo onse unalipiridwa motero kuti ubale pakati pa munthu ndi Mulungu ukhala wokonzedwanso kapena kuti umayambanso mwa Yesu cifukwa ca imfayo (Ahebri 9:11-14; 10:10; Aroma 5:8; 6:23).
Cikristu ciphunzitsa kuti cofunikira kuti munthu apulumutsidwe ndi kulowa kumwamba, munthuyo ayenera kuika cikhulupiriro cake conse mwa Yesu Kristu ndi nchito yonse imene Yesu anaicita pamtanda. Ngati munthu akhulupira kuti Yesu anamufera nalipira mlandu wa macimo ake a munthuyo, naukitsidwa, ndiko kuti munthuyo apulumutsidwa. Palibe cinthu cimene munthu wina aliyense angacite kulandira cipulumutso. Palibe amene angathe kukhala “wabwino kwambiri” kuti angakondweretse Mulungu pa iye yekha cifukwa ife tonse ndife ocimwa (Yesaya 53:6; 64:6-7). Caciwiri, palibe cina cimene tiyenera kucita cifukwa Yesu Kristu anacita kale nchito yonse yacipulumutso! Pamene Iye anali pa mtanda anati, “Kwatha” (Yohane 19:30), kutanthauza kuti anatsiriza nchito yonse ya cipulumutso ca anthu.
Dziwani kuti palibe cinthu cina ciriconse cimene wina angacite kuti alandire cipulumutso, pamene munthu waika cikhulupiriro cace mu nchito ya Kristu yocitika pa mtanda, palibenso cimene wina anacite kutaya cipulumutso cake cifukwa mwina cakuti nchito inacitika ndi Yesu ndipo Iyeyo anaitsiriza. Cipulumutso sicigona pa iye wakucilandira koma pa Iye amene amacipereka. Pa Yohane 10:27-29 pali mau awa, “Nkhosa zanga zimva mau anga, ndipo Ine ndizizindikira, ndipo zinditsata Ine. Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzaonongeka ku nthawi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m'dzanja langa, Atate wanga, amene anandipatsa izo, ali wamkulu ndi onse; ndipo palibe wina angathe kuzikwatula m'dzanja la Atate.”
Anthu ena atha kuganiza kuti, “Zimenezo ndizabwino – ndikangokhulupira ndi kupulumutsidwa pambuyo pake ndingacite ciriconse condikomera mosataya cipulumutsoco!” Monga mwa Cikristu, cipulumutso sicikhala comangidwa pa moyo wakale ai. Koma cipulumutso cidzetsa ufulu wakulekanitsa munthu kukhala kapolo wa macimo ndi kumuyambitsa kukhala pa ubale ndi Mulungu. Pamene kalero tinali akapolo aucimo, tsopano tikhala akaopolo a Kristu (Aroma 6:15-22). Padziko lapansi pano, okhulupirira onse malinga alipano ndi thupi la umuthu adzakumanabe ndi kulimbana ndi macimo. Koma ngakhale ziri tero, Akristu ali ndi cigonjetso ca ucimo powerenga ndi kuyenda mu Mau a Mulungu mu umoyo wao wa tsiku ndi tsiku komanso potsogozedwa ndi Mzimu Woyera – kuzipereka kuti Mzimu Woyera awatsogolere pa zonse za umoyo.
Motero pamene zipembedzo zina zaima pa zocita ndi zosacita ndi kutsata malamulo cabe, Cikristu cagona pakukhulupirira Yesu kuti mwa imfa yace ndi kuukitsidwa kwace munthu aomboledwa cifukwa m’menemo macimo ake anakhululukiridwa. Mlandu wa macimo athu unalipiridwa ndipo titha kukhala m’ciyanjano ndi Mulungu. Titha kukhala opambana cifukwa tili ndi cigonjetso ca macimo, ndipo titha kuyenda m’ciyanjano ndi Mulungu ndi kumvera Iye. Ico ndico ciphunzitso coona ceniceni ca Cikristu.
English
Kodi Cikristu nciani ndipo Akristu amakhulupirira ciani?