settings icon
share icon
Funso

Kodi Akristu ayenera kumvera lamulo la mu Cipangano Cakale?

Yankho


Kumvetsa za mfundo iyi, muyenera kudziwa kuti malamulo a Chipangano Cakale anapatsidwa kwa dziko la Aisrayeli osati kwa Akristu. Malamulo ena anapatsidwa kuonetsa m’mene iwo angamverere ndi kuyamikira Mulungu (mwa citsanzo, Malamulo Khumi). Malamulo ena onaonetsa ndi kudziwitsa Aisrayeli mopempherera ndi moperekera nsembe atacimwa. Malamulo ena anaonetsa kusiyana kwa Aisrayeli ndi mitundu ina (zakudya zao ndi kabvalidwe kao). Palibe ngakhale imodzi mwa malamulo amenewo ikhuza a Kristu lero. Pamene Yesu anafa pa mtanda anathetsa cilamulo conse ca M’cipangano Cakale (Aroma 10:4; Agalatiya 3:23–25; Aefeso 2:15).

M’malo mwa cilamulo ca M’cipangano Cakale, tili pansi pa lamulo la Kristu (Agalatiya 6:2), imene ikuti, “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse…ndipo uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini” (Mateyu 22:37-39). Ngati titsatira malamulo awiriwa, tidzakwaniritsa cimene Kristu afuna kucokera kwa ife: “Pa malamulo awa awiri mpokolowekapo cilamulo conse ndi aneneri” (Mateyu 22:40). Tsopano sindiko kunena kuti Cilamulo ca M’cipangano Cakale ndi copanda nchito lero ai. Malamulo ambiri Mcipangano Cakale akugwa pa gawo la “kukonda Mulungu” ndi “kukondana wina ndi mzace.” Cilamulo ca M’cipangano Cakale cionetsa bwino kwambiri m’mene tifunikira kukondera Mulungu komanso zofunikira pokonda mzathu. Pa nthawi imodzimodzi kunena kuti Cilamulo ca M’cipangano Cakale ciyenera Akristu lero, ndi kulakwitsa. Cilamulo ca M’cipangano Cakale ndi mbali imodzi la buku lonse (Yakobo 2:10). Zikhoza kukhala kuti conse citikhuza, kapena conse sicitikhuza. Ngati Yesu anakwaniritsa cabe mbali ina ya cilamulo, monga mwakuzipereka nsembe, ndiko kuti Iye anakwaniritsa zonse.

“Pakuti ici ndi cikondi ca Mulungu, kuti tisunge malamulo ace: ndipo malamulo ace sali olemetsa” (1 Yohane 5:3). Malamulo Khumi aja ndi cimangirizo cofunikira pa umoyo ca malamulo onse a Cipangano Cakale. Pakati pa malamulo amenewo, malamulo asanu ndi anai (9) awabwerezanso ku Cipangano Catsopano (onse kucotsako cabe lamulo la kukumbukira Sabata). Ndicodziwikiratu kuti ngati tikonda Mulungu wathu, sitidzalola kupembedza milungu ina yacabecabe kapena kuigwadira iyo. Ngati tikonda anansi (a neba), sitidzawapha iwo, kapena kuwanamiza, kucita nao zogonana-gonana (kapena kukhala pa cibwenzi cobisika) kapena kusilira zimene ali nazo. Colinga ca lamulo la m’Cipangano Cakale ndi kutitsutsa ife anthu za kulephera kwathu kusunga malamulo ndi kutionetsa ife anthu Yesu Kristu ngati Mpulumutsi (Aroma 7:7-9; Agalatiya 3:24). Lamulo la m’Cipangano Cakale, sanaliikeko kuti likhale lokhudza anthu ku dziko lonse mu nthawi zonse ai. Ife tiyenera kukonda Mulungu wathu ndi kukondana ndi abale. Tikakhulupira malamulo awiriwo mokhulupiririka, tidzagwira zonse zimene Mulungu afuna kucokera kwa ife.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi Akristu ayenera kumvera lamulo la mu Cipangano Cakale?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries