Funso
Kodi m’Khristu ndi chiyani?
Yankho
Tanthauzo la m’Khristu mu buku lopereka matanthauzo a mawu osiyanasiyana (dikishonale) likhonza kukhala china chake chofanana ndi “munthu wonena poyera za chikhulupiliro chake mwa Yesu monga Khristu kapena mumpingo potsatira zophunzitsa za Yesu.” Pamene iyi ili mfundo yabwino yoyambira, monga m’mene madikishonale ambiri akutanthauzira, pena pake sizilumikiza bwinobwino choonadi cha tanthauzo la m’Khristu lamu Baibulo. Mawu oti “m’Khristu” anagwiritsidwa ntchito katatu ku chipangano chatsopano (Machitidwe a Atumwi 11:26; 26:28; 1 Peturo 4:16). Otsatira ake a Yesu Khristu poyambilira amatchulidwa kuti “Akhristu” ku Antioch (Machitidwe a Atumwi 11:26) chifukwa khalidwe lawo, zochitika, ndi zolankhula zawo zinali ngati Khristu. Mau akuti “Mkhristu” amatanthauza, “kukhala wa bungwe la Khristu” kapena “wotsatira wake wa Khristu.”
Mwatsoka nthawi itadutsa, mau oti “m’Khristu” atha mphamvu ya cholinga chake ndipo amakonda kugwiritsidwa ntchito kwa munthu amene ali wa chipembedzo kapena otchuka koma amene ali kapena asali wotsatira wake wa Yesu Khristu. Anthu ambiri amene sakhulupilira mwa Yesu Khristu amadziyesa a Khristu chifukwa chakuti amapita ku tchilitchi kapena amakhala m’dziko la a Khristu. Koma kupita ku tchalitchi, kutumikira iwo amene ali ofooka muuzimu kuposa inu, kapena kukhala munthu wabwino sikungakupangeni inu kukhala m’Khristu.
Baibulo limaphunzitsa kuti ntchito zabwino zimene timapanga sizingatipangitse kuti Mulungu atilandire. Tito 3:5 akunena kuti, “Anatiwombola, osati chifukwa cha zabwino zimene tachita, koma chifukwa cha chifundo chake. Anatiwombola kudzera m’kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera.” Kotero, m’Khristu ndi munthu amene anabadwanso mwatsopano mwa Mulungu (Yohane 3:3; Yohane 3:7; 1 Peturo 1:23) ndipo wayika chikhulupiliro chake mwa yesu Khristu. Aefeso 2:8 amatiuza kuti ndi “… mwa chisomo mwapulumutsidwa, kudzera m’chikhulupiliro – ndipo ichi sichichokera kwa inu, ndi mphatso ya kwa Mulungu.”
M’khristu weniweni ndi munthu amene waika chikhulupiliro mu umunthu komanso ntchito zake za Yesu khristu, kuphatikizapo imfa yake pamtanda ngati malipiro a machimo athu ndi kuuka kwake pa tsiku lachitatu. Yohane 1:12 amatiuza kuti, “Koma onse amene anamulandira Iye, kwa iwo amene akhulupilira mu dzina lake, anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu.” Chizindikiro cha m’Khristu weniweni ndi kukonda ena ndikumvera Mawu a Mulungu (1 Yohane 2:4, 10). M’khristu weniweni ndiyedi mwana wa Mulungu, gawo la banja lenileni la Mulungu, ndi m’modzi amene wapatsidwa moyo watsopano mwa Yesu Khristu.
Kodi mwapanga ganizo la Khristu chifukwa cha zimene mwawerenga pano? Ngati ndi choncho, chonde sindikizani batani la “Ndavomera kulandira Khristu lero” pansipa.
English
Kodi m’Khristu ndi chiyani?