settings icon
share icon
Funso

Kodi mkazi wa Kaini anali ndani? Kodi mkazi wa Kaini anali mlongo wace?

Yankho


Baibulo silifotokoza kwenikweni za mkazi wa Kaini kuti anali ndani. Yankho limene tingathe kuganizira ndi lakuti mkazi wa Kaini anali mlongo wace kapena mwana wamkazi wa mlongo wace kapena mwana wa mkazi wa mcimwene wace, kapena wina wace. Baibulo silifotokozanso kuti Kaini anali ndi zaka zingati pamene anapha mcemwene wace Abele (Genesis 4:8). Pakuti onse anali alimi, cioneka kuti onse anali akulu-akulu mwina amabanja ao. Adamu ndi Hava, sanali cabe ndi ana awiri, Kaini ndi Abele, koma analinso ndi ana ena pa nthawi imene Kaini anapha Abele. Ndipo patsogolo pace anakhalanso ndi ana ena ambiri (Genesis 5:4). Cifukwa cakuti Kaini anacita mantha ndi umoyo wace atapha Abele (Genesis 4:14) cionetseratu kuti panalinso ana ena mwina ena a iwo anali adzukulu a Adamu ndi Hava amene analiko kale pa nthawiyo. Mkazi wa Kaini (Genesis 4:17) anali mwana kapena m’dzukulu wa Adamu ndi Hava.

Pakuti Adamu ndi Hava anali anthu woyamba, ano ao analibe umwai wosankha koma kungokwatirana. Pa nthawiyo Mulungu sanaletse cikwati ca mabanja kufikira nthawi yina yace patsogolo pamene anthu anaculuka kwambiri motero kuti kukwatirana kwa pa banja limodzi sikunali kofunikanso (Levitiko 18:6-18). Vuto ndi lakuti kukwatirana pacibale masiku ano (mwacitsanzo, mcemwene ndi mcemwali (mlongo)) awiriwo atha kukhala ndi matenda opezeka cabe m’magazi ao ndipo pamenepo cikhala cidziwika kuti ana obadwa atenga matendawo kucokera kwa makolo onse awiri, motero pakhala ciopsezo cacikulu ca matenda kwa iwo. Ngati anthu awiri akwatirana kucokera ku mabanja osiyana, ana ao satengera zonse za magazi akholo limodzi ai koma atengera za makolo awiriwo moteronso amakhala olimba ku matenda ena. Codziwika ndi cakuti anthu pamene abalana zambiri za iwo zisinthika ndipo zisintho zimenezo zipatsilidwa mu midadwo yao. Zonse zokhuzana ndi matupi a Adamu ndi Hava zinali cabe bwino, analibe matenda ndipo mwazi wao unali monga Mulungu anafunira powalenga iwo. Cifukwa ca ico, ana ao komanso amene anabwadwa potsatira iwo ndi ena anali ndi matupi abwino komanso olimba koposa matupi athu lero lino. Ana a Adamu ndi Hava ngati anali ndi zovuta m’magazi ao, ngati zinalipo zinali zocepa. Motero kukwatirana pa ubale kunali bwino.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi mkazi wa Kaini anali ndani? Kodi mkazi wa Kaini anali mlongo wace?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries