Funso
Kodi mphatso yakulankhula mu malilime ndi ciani?
Yankho
Kulankhula m’malilime koyamba kunacitika pa tsiku lija la Pentekoste monga tiwerenga pa Macitidwe 2:1-4. Atumwi anapita kukagawana Mau a Mulungu ndi unyinji wa anthu, kulankhula kwa iwo m’cilankhulo caocao anthuwo: “Akrete, ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m'malilime athu zazikuru za Mulungu” (Macitidwe 2:11). Mauwa, onena kuti “malilime” mu Cigiriki atanthauza kuti “zilankhulo.” Motero mphatso ya kulankhula m’malilime ndi kulankhula cilankhulo cina pofuna kufalitsa Mau a Mulungu kwa munthuyo kuti amve conenedwaco. Mu 1 Akorinto pa machapitala a 12-14, Paulo alankhula za mphatso zodabwitsa zambiri ndipo iye akuti, “Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikakupindulitsani ciani, ngati sindilankhui landi inu kapena m'bvumbulutso, kapena m'cidziwitso, kapena m'cinenero, kapena m'ciphunzitso” (1 Akorinto 14:6). Monga mwa mtumwi Paulo, mogwirizana ndi mau onena za malilime pa Macitidwe 2, kulankhula malilime kukhala kothandiza kwa iye wakumva Mau a Mulungu m’cilankhulo cake, ndipo saphindulitsa wina aliyense pokhapo mauwo amasulilidwa.
Munthu wopatsidwa mphato yakumasulira malilime (1 Akorinto 12:39) atha kumvetsa ndi kudziwa cymene wolankhula m’malilime anali kulankhula ngakhale kuti iye sadziwa cilankhuloco. Iye womasulira kulankhula mwa malilime ameneyo ndiye amauza anthu ena cymene wolankhula m’malilime amanena, kuti aliyense pamalopo adziwe ndi kumvetsa. “Cifukwa cace wolankhula lilime, apemphere kuti amasule” (1 Akorinto 14:13). Potsiliza, cimangirizo ca Pulo pokhuzana ndi kumasulira kwa malilime kumveka bwino pa mau awa “koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi cidziwitso canga, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m'lilime” (1 Akorinto14:19).
Kodi mphatso ya kulankhula mu malilime ndi yofunikira lero. Coyamba 1 Akorinto 13:8 anena kuti mphatso imeneyi yakulankhula inatha, ngakhale kuti kutha kwakeku kulumikizidwa ndi kutha kwa kufika kwa “cangwiro” mu 1 Akorinto 13:10. Ena amanena za kusiyana mukagwiritsidwe nchito ka liu la mu ci Giriki lokhuza za cinenero ndi nzeru “kutha” ndi kuti “malilime anatha” kukhala ngati umboni wa kutha kwa kulankhula m’malilime asanafike “wangwiroyo”. Ngakhale kuti zitha kukhala tero koma ici sicitsimikiza tero ai monga mwa mau opezeka pomwepo. Ena amanena za mau ena opezeka monga pa Yesaya 28:11 ndi Yoweli 2:28-29 kukhala ngati umboni wakuti kulankhula m’malilime cinali cizindikiro cakubwera kwa ciweruzo cymene Mulungu waika mtsogolo. Pa 1 Akorinto 14:22 anena za malilibe kukhala ngati “cizindikiro kwa osakhulupirira.” Kulingana ndi kutsutsa kumeneku, mphatso yakulankhula m’malilime inali cenjezo kwa Ayuda kuti Mulungu adzaweruza Aisrayeli cifukwa ca kukana kubvomereza kuti Yesu Kristu ndiye Mesiya. Motero, Mulungu analangadi Aisrayeli pamene (Aroma anafika ndi kuwonongeratu tauni yonse ya Yerusalemu kuphatikizapo kacisi wakomweko mu caka ca AD 70), ndiye pamenepo mphatso ya kulankhula m’malilime siitha kugwira nchito yake pa cifukwa cimeneco. Ngakhale kuti ciganizo ici ndi cotheka ndithu, colinga cakukwaniritsa kulankhula m’malilime sicigona pothetsa kapena kulankhula cabe. Mau a Mulungu, sanena moika cidindo kuti mphatso yakulankhula m’malilime inayatha kapena kuti yatha.
Pa nthawi imodzimodzi, ngati mphatso yakulankhula m’malilime inali yocitacita mu mpingo lero, ikadacitika mogwirizana ndi Mau a Mulungu monga mwa zolembeka mu Baibulo. Kulankhula kumeneko kukadakhala cilankhulo coonadi ndi copatsa nzeru (1 Akorinto 14:10). Colinga cake cikadakhala cakufikiritsa Mau a Mulungu kwa munthu wina amene alankhula cilankhulo cina (Macitidwe 2:6-12). Zotero zikadakhala zogwirizana ndi lamulo limene Mulungu anapereka kwa mtumwi Paulo “Ngati wina alankhula lilime, acite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire. Koma ngati palibe womasulira, akhale cete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu” (1 Akorinto 14:27-28). Zikadakhalanso zogwirizana ndi mau apa 1 Akorinto 14:33 “pakuti Mulungu sali Mulungu wa cisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.”
Ndi kotheka ndithu kuti Mulungu akhoza kupatsa wina mphatso ya kulankhula malilime kuti munthuyo alumikizane ndi wina m’cilankhulo cinaco. Mzimu Woyear amacita monga mwakufuna kwace pakupereka mphatso ya zauzimu (1 Akorinto 12:11). Tangoganizirani kuti cinakakhala bwanji anthu anchito za umishoni iwowo akadapatsidwa mphamvu ndi mphatso imeneyi, mosapita kusukula la cilankhulo, koma kuti nthawi yomweyo anafika pamalo, pomwepo basi ndikulankhula cilankhulo ca anthuwo kapena kuti nzika. Koma cioneka kuti Mulungu sacita tero ai. Malilime aoneka kuti kulibe lero monga m’mene ankacitikira mu Cipangano Catsopano, ngakhale kuti zitakhale tero cikhoza kukhala cinthu cothandiza kwambiri. Ambiri a okhulupirira amene iwo akuti alankhula m’malilime, sagwirizana ndi momwe Mau a Mulungu anenera pa nkhaniyi. Mfundo za coonadi izi zithat kutanthauza kuti mphatso yakulankhulu m’malilime kulibe kapena kuti siyopezeka mu pulano ya Mulungu pakati pa mpingo wake lero.
English
Kodi mphatso yakulankhula mu malilime ndi ciani?