settings icon
share icon
Funso

Kodi baibulo liphunzitsa ciani za Mulungu m’modzi mwa atatu?

Yankho


Covutitsa kwenikweni pa ciphunzitso ca ci Kristu cokhuza za nkhani ya Mulungu m’modzi mwa atatu ndi cakuti palibe kumasulira kumene kutha kucitika mokwanira kapena mofikapo ndithu. Motero, akamanena za Mulungu m’modzi mwa Atatu, ciphunzitso cimeneco cikhala covuta kwa munthu wina aliyense kumvetsa ndipo pambyo pake kumasulira ciphunzitsoco. Mulungu ndi wamkuru ndi woposa ife, tisayembekezere kuti tidzatha kudziwa ndi kumvetsa bwinobwino zace zonse. Baibulo liphunzitsa kuti Atate ndiye Mulungu, ndi kuti Yesu ndiye Mulungu, ndiponso kuti Mzimu Woyera ndiye Mulungu. Baibulo liphunzitsanso kuti pali cabe Mulungu m’modzi. Ndipo poyesa kumvetsa mwina titha kumvetsa mwa kumasulira za ubale umenewu wa pakati pa atutuwo, okhala Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera koma si capafupi kumvetsa mwa nzeru za umuthu wathu. Cimeneci, kusamvetsa kwathu, sikutanthauza kuti ciphunzitso ca Mulungu m’modzi mwa atatu ndi conama kapena kuti cabodza kapenso kuti sicigwirizana ndi Mau a Mulungu.

Mulungu ndi m’modzi koma mwakudzionetsera mwa anthu atatu – Mulungu m’modzi mwa Atatu. Kumvetsa zimenezi sindiko kutanthauza kuti pali milungu itatu ai. Conde sungani kapena kumbukiranai kuti pamene tiona pa gawo kapena ciphunzitso ici, tikamanena za “Mulungu m’modzi mwa Atatu” mauwo sapezeka mu Baibulo. Liu limenelo limagwiritsidwa nchito poyesetsa kuti timvetse za Mulungu m’modzi mwa atatu – cikhalidwe cace pakati pa Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera amene ali Mulungu m’modzi. Cofunika kudziwa ndicakuti mau amenewa akuti, Mulungu m’modzi mwa Atatu sapezeka mu Baibulo. Ndipo ici ndi cimene Mau a Mulungu anena pa zokhuza Mulungu m’modzi mwa Atatu:

1) Pali cabe Mulungu m’modzi (Deuteronomo 6:4; 1 Akorinto 8:4; Agalatiya 3:20; 1 Timoteo 2:5).

2) Mulungu m’modzi mwa atatu ndi mau akunena, Mulungu Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera (Genesis 1:1, 26; 3:22; 11:7; Yesaya 6:8; 48:16; 61:1; Mateyu 3:16-17; 28:19; 2 Akorinto 13:14). Mu buku la Genesis 1:1, ndi mau amu CiHebri oculukitsa Elohimu agwiritsidwa nchito pamenepo. Pa Genesis 1:26, 3:22, 11:7 ndi Yesaya 6:8, pali kuculukitsa kwa m’lowa m’malo wonena kuti “ife” akugwiritsidwa nchito pomwepo. Liu lakuti Elohimu ndi m’lowa m’malo woculukitsidwe oti, “ife” mu Cihebri anena za anthu opitilira pa m’modzi. Koma cilingo ici si Mfundo yokolowekapo nkhani ya Mulungu m’modzi mwa Atatu, koma ionetsa kuculuka ndithu mwa Mulungu. Liu la mu Cihebri lakuti Elohimu, ndithudi linena za Mulungu m’modzi mwa atatu.

Pa Yesaya 48:16 ndi 61:1, Mwana akulankhula ndi kulumikiza Mulungu Atate ndi Mzimu Woyera. Linganizani ndi mau opezeka pa Yesaya 61:1 ndi mau apa Luka 4:14-19 kuona kuti akulankhulayo ndi mwana. Pa Mateyu 3:16-17 akunena za zimene zinacitika pa ubatizo wa Yesu. Cooneka pamenepa ndi kutsika kwa Mulungu Mzimu Woyera, kutsikira pa Mulungu Mwana ndipo Mulungu Atate pamenepo akulankhula mau akukondwera ndi Mwana wakeyo. Pa Mateyu 28:19 ndi 2 Akorinto 13:14 pamenepo pali zitsanzo za Mulungu m’modzi mwa Atatu, kuonetsa kufanana ndi umodzi wao.

3) Mau ambiri afotokoza kusiya pakati pa Membala ali yense wa Mulungu m’modzi mwa Atatu. M’cipangano Cakale, “AMBUYE” asiyana ndi “Ambuye” (Genesis 19:24; Hoseya 1:4). AMBUYE ali ndi Mwana (Masalmo 2:7; Miyambo 30:2-4). Ndipo Mzimu asiyana ndi “AMBUYE” (Numeri 27:18) komanso asiyana ndi “Mulungu” (Masalmo 51:10-12). Mulungu Mwana asiyanitsidwa ndi Mulungu Atate (Masalmo 45:6-7; Ahebri 1:8-9). M’cipangano Catsopano, Yesu anena za Atate kuti adatumiza Mthandizi, Mzimu Woyera (Yohane 14:16-17). Izi zionekeratu kuti Yesu sanadziyese kukhala Atate kapena kukhala Mzimu Woyera. Taonani ndi kuganizirapo pa nthawi zonse mu Mauthenga abwino pamene Yesu alankhula kwa Mulungu Atate. Kodi pamenepo amalankhula kwa Iye yekha? Ai. Amalankhula ndi wina mwa Mulungu m’modzi mwa Atatu – Atate.

4) Membala ali yense wa Mulungu m’modzi mwa Atatu ndi Mulungu. Atate ndiye Mulungu (Yohane 6:27; Aroma 1:7; 1 Petro 1:2). Mwana ndiye Mulungu (Yohane 1:1, 14; Aroma 9:5; Akolose 2:9; Ahebri 1:8; 1 Yohane 5:20). Mzimu Woyera ndi Mulungu (Macitidwe 5:3-4; 1 Akorinto 3:16).

5) Pali kugwirizana ndi kumvana kwakukuru pakati pa Atate, Mwana ndi Mzimu Wouyera. Mau a mu Baibulo atiuza kuti Mzimu Woyera amamvera Atate ndi Mwana, ndipo Mwana amamveranso Atate. Ici ndicikhalidwe ndi ubale wao (Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera) zimenenso zionetsa umulungu wao komanso umodzi mwa Mulungu m’modzi mwa Atatu. Izi ndi zinthu zapafupi, koma nzeru zanthu ngati anthu singathe kulondola ndi kumvetsa zonsezi zokhuza Mulungu wamuyaya. Kunena zokhuza Mwana, onani pa Luka 22:42, Yohane 5:36, Yohane 20:21, ndi 1 Yohane 4:14. Ndipo kuona pa zokhuza Mzimu Woyera, onani pa Yohane14:16, 14:26, 15:26, 16:7, makamaka pa mau apa Yohane 16:13-14.

6) Mamembala onse a Mulungu m’modzi mwa Atatu, (Mulungu Atate, Mulungu Mwna ndi Mulungu Mzimu Woyera) onsewo ali ndi nchito zosiyanasiyana. Atate ndiye wodzetsa cilengedwe conse (1 Akorinto 8:6; Chibvumbulutso 4:11); cionetso ca zaumulungu (Chibvumbulutso 1:1); cipulumutso (Yohane 3:16-17); ndi nchito za Yesu panthawi yakuonekera kwace mwa umuthu pa dziko (Yohane 5:17; 14:10). Atate ndiye amene amayambitsa zonsezi. v Mwana ndiye njira m’mene Mulungu Atate acita zinchito izi. cilengedwe ca dziko ndi kasamaliro cace (1 Akorinto 8:6; Yohane 1:3; Akolose 1:16-17); cionetso ca zaumulungu (Yohane 1:1; 16:12-15; Mateyu 11:27; Chibvumbulutso 1:1); ndi cipulumutso (2 Akorinto 5:19; Mateyu 1:21; Yohane 4:42). Mulungu Atate acita zonsezi kupyolera mwa Mwana wace amene akhala ngati wocita nchitoyo.

Mzimu Woyera ndiye njira m’mene Mulungu Atate acita zinchito izi: cilengedwe ca dziko ndi kasamaliro cace (Genesis 1:2; Yobu 26:13; Masalmo 104:30); cionetso ca zaumulungu (Yohane 16:12-15; Aefeso 3:5; 2 Petro 1:21); ndi cipulumutso (Yohane 3:6; Tito 3:5; 1 Petro 1:2); ndi nchito za Yesu (Yesaya 61:1; Macitidwe 10:38). Mwa mphamvu ya Mzimu Woyera, Atate acita zonse.

Pakhala pakukhala kuyesayesa mwa njira zambiri kukhala ndi zitsanzo za kumasulira za Mulungu m’modzi mwa Atatu. Koma ngakhale zitsanzo zodziwika bwino kwambiri, zonsezo zakhala zoperewera kufotokozera bwino. Dzira likhala ndi cikhokho ndipo pali cam’kati cace coyera komanso m’kati mwace muli cacikasu, zonsezo ndi zigawa za dzira limodzi. Kuziika pazokha sizikhala dzira ai. Tikhozanso kuona pa zitsanzo zina zimene ziri ndi zigawo zingapo monga zipatso zokhala ndi khungu lakubwalo, camkati ndi njere (mbewu) zake. Zigawozo pazokha sizipanga cipatsoco. Motero Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera si zigawo za Mulungu; wina aliyense wa iwowa ndi Mulungu. Ngati munamvapo za citsanzo ca madzi, cimeneco cimvekako bwino koma cilepheranso kumasulira za Mulungu m’modzi mwa Atatu. Madzi-madzi, nthunzi, ndi madzi oundana kapena matalala zonsezo ndi madzi koma mu zigawo zina kapena m’maonekedwe ena. Motero Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera si zigawo za Mulungu, yense wa iwowa ndi Mulungu. Zitsanzo zimenezi zingotithandiza cabe kuti tikhale ndi cithunzi koma sikuti zonsezo zimasulidwa bwino ai komanso si zokwanira bwino kuti tikhoza kumvetsa. Mulungu wamuyaya sangathe kumasuliridwa kapena kufotokozedwa mofikapo ndi nzeru za munthu ai.

Ciphunzitso ca Mulungu m’modzi mwa Atatu cakhala cobvuta kumvetsa motero kuti pakati pa anthu ambiri, Akristu, pakhala kugawanikana kuyambira zaka zambiri zakumbuyo. Koma ndicodziwikabe kuti zigawo za Mulungu m’modzi mwa Atatu ziri mu Mau a Mulungu ndipo ndizofotokozedwa bwinobwino. M’menemo tidziwa kuti, Atate ndi Mulungu, Mwana ndi Mulungu, ndipo Mzimu Woyera ndi Mulungu – koma pali cabe Mulungu m’modzi. Cimeneco ndico ciphunzitso copezeka mu Baibulo cokhuza Mulungu m’modzi mwa Atatu. Kupitilira apo, ndiko kuti nkhaniyo ndiyovuta, ndipo pakhoza kukhala kusiyana maganizo kotheratu. M’malo motsutsana ndi kufuna kupeza tanthauzo la mau amenewa akuti, Mulungu m’modzi mwa Atatu, tiyenera kumvetsetsa kuti sitikhoza kumasulira zonse za Mulungu monga mwa nzeru zathu za umunthu, ife tiyenera kuona pa ziphunzitso zace ndi ukulu wace cabe. “Ha! kuya kwace kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwace kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ace, ndi njira zace nzosalondoleka! Pakuti anadziwitsa ndani mtima wace wa Ambuye? Kapena anakhala mphungu wace ndani?” (Aroma 11:33-34).

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi baibulo liphunzitsa ciani za Mulungu m’modzi mwa atatu?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries