Funso
Kodi citanthauza ciani kukhala Mkristu wobadwa kwa tsopano? Kodi ndingabadwe bwanji kwa tsopano?
Yankho
Kodi citanthauza ciani kukhala Mkristu wobadwa kwa tsopano? Nkhani imene iyankha funso limeneli mu Baibulo ili pa Yohane 3:1-21. Ambuye Yesu Kristu akulankhula ndi Nikodemo, m’modzi wa Afarisi komanso wokhala membala wa Sanihedrini (gulu lotsogolera Ayuda). Nikodemo anafika kwa Yesu usiku ndi mafunso.
Ndipo pamene Yesu anali kulankhula ndi Nikodemo, Iye anati, “Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu. Nikodemo ananena kwa Iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m'mimba ya amace ndi kubadwa? Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu. Cobadwa m'thupi cikhala thupi, ndipo cobadwa mwa Mzimu, cikhala mzimu. Usadabwe cifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwatsopano” (Yohane 3:3-7).
Mau akuti “kubadwa mwatsopano” atanthauza “kubadwa kucokera kumwamba.” Nikodemo anafunadi thandizo lenileni. Iye anafuna cisintho ca mtima wace – akhale ndi mzimu woyanjana ndi Mulungu. Kubadwanso, kubadwa kwatsopano, ndi nchito imene Mulungu amacita mu umoyo wa munthu okhulupirira, kumupatsa iye umoyo wosatha (2 Akorinto 5:17; Tito 3:5; 1 Petro 1:3; 1 Yohane 2:29; 3:9; 4:7; 5:1-4, 18). Yohane 1:12, 13 akutero kuti, “kubadwa kwatsopano” komanso tingathe kunena kuti kutero ndi “kukhala ana a Mulungu” mwa kukhulupirira mdzina la Yesu Kristu.
Funso linafunsidwa mwa nzeru ndithu kuti, “Ncifukwa ninji munthu ayenera kubadwa mwa tsopano?”Mtumwi Paulo polemba akunena tere pa Aefeso 2:1, “Ndipo inu, anakupatsani moyo, pokhala munali akufa ndi zolakwa, ndi zocimwa zanu.” Ndipo kwa Aroma anati, “pakuti onse anacimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu” (Aroma 3:23). Anthu ocimwa akhala “akufa mu mzimu”; akalandira moyo pokhulupirira mwa Yesu Kristu pamenepo iwo akhala obwadwa mwatsopano. Okhwao amene abatdwa mwatsopano, ndiwo amene macimo awo amakhululukidwa nakhala mu ubale ndi Mulungu.
Kodi cimeneco cimacitika bwanji? Aefeso 2:8-9, akuti, “Pakuti muli opulumutsidwa ndi cisomo cakucita mwa cikhulupiriro, ndipo ici cosacokera kwa inu: ciri mphatso ya Mulungu; cosacokera ku nchito, kuti asadzitamandire munthu ali yense” pamene wina wapulumutsidwa, iye akhala wobadwa kwa tsopano, mzimu wake utasinthikanso kukhala watsopano, ndipo tsopano iye akhala mwana wa Mulungu pokhala iye wobadwa kwa tsopano. Mwakukhulupirira Yesu Kristu, Iye amene analipira cilango ca macimo, pakufa pa mtanda, ameneyo ndiye “amabwdwitsa kwa tsopano.” “Cifukwa cace ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano” (2 Akorinto 5:17).
Ngati mukalibe kukhulupirira mwa Ambuye Yesu Kristu ngati Mpulumutsi wanu, muyenera kuganizirapo pa cimene Mzimu Woyera amalankhula ndi inu mu mtima mwanu? Muyenera kukhala munthu wobadwa mwatsopano. Mudzapemphera pemphero la kulapa ndi kukhala wolengedwa watsopano mwa Kristu lero lino. “Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lace; amene sanabadwa ndi mwazi, kapena ndi cifuniro ca thupi, kapena ndi cifuniro ca munthu, koma ca Mulungu” (Yohane 1:12-13).
Ngati ufuna kubvomereza ndi kulandira Yesu Kristu ngati Mpulumutsi ndi kubadwa kwa tsopano, pano pali pemphero limene mungathe kunena kapena kupemphera mokhulupirira ndithu. Kumbukirani kuti kunena pempherid ili kapena pemphero lina lirilonse sikungathe kukupulumutsani ai. Ndi kukhulupira Yesu cabe kumene kungathe kukupulumutsani ndi kucotsa macimo anu. Pemphero ili ndi njira cabe yoonetsa kuti cikhulupiriro canu ciri mwa Mulungu ndi kumuyamika Iye popereka cipulumutso kwa inu. “Mulungu, ndidziwa kuti ndakucimwirani ndipo ndiyenera cilango cosatha. Koma Yesu Kristu anatenga cilango cimeneco m’malo mwa ine ndipo mwa Iye ndikhululukidwa macimo anga onse. Ndaika cikhulupiriro canga ndi cipulumutso canga mwa Inu. Zikomo cifukwa ca cisomo canu ndi cikhululukiro ca macimo – cimene ciri mphatso la moyo wosatha! Amen!”
Kodi mwapanga ganizo la Khristu chifukwa cha zimene mwawerenga pano? Ngati ndi choncho, chonde sindikizani batani la “Ndavomera kulandira Khristu lero” pansipa.
English
Kodi citanthauza ciani kukhala Mkristu wobadwa kwa tsopano? Kodi ndingabadwe bwanji kwa tsopano?