settings icon
share icon
Funso

Kodi Yesu ndiye njira yokha yopita Kumwamba?

Yankho


Inde, Yesu ndiye njira yokhayo yopita kumwamba. Mau otero mwina sakhoza kulandiridwa m’makutu ya anthu ena makamaka m’masiku ano pamene anthu akukhulupirira za maphunziro, koma coonadi ndi cakuti, Yesu yekhayo ndiye njira. Baibulo iphunzitsa kuti palibe njira ina yacipulumutso koma kupyolera mwa Yesu. Mu buku la Yohane 14:6, Yesu akutero kuti, “Ine ndine njira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.” Iye si ndiye njira kuti mwina zilipo zambiri, ai, Iye yekha ndiye njira yokhayo imodzi. Inde palibe munthu ngakhale m’modzi, wakhalidwe labwino, kapena wopambana pa zambiri, kapena wa nzeru zakuya, kapena wolungama mwa iye yekha, amene angathe kufika kwa Mulungu koposa kudzera mwa Yesu.

Yesu ndiye njira yokha yopita kumwamba pa zifukwa zambirimbiri. Yesu “anasankhidwa ndi Mulungu” kukhala Mpulumutsi (1 Petro 2:4). Yesu ndi yekhayo amene anatsika kucoka kumwamba ndi kubwereranso (Yohane 3:13). Wokhala ndi maonekedwa a umuthu ndi yekhayo amene anakhala kopanda cimo lina liri lonse mu umoyo wace padziko (Ahebri 4:15). Iyeyo ndiye nsembe ya macimo (1 Yohane 2:2); Ahebri 10:26). Pamene Iye anadza kudziko anakwaniritsa lamulo ndi aneneri (Mateyu 5:17). Iye ndiye munthu yekha amene anagonjetsa imfa motheratu (Ahebri 2:14-15). Iye ndiye Mkhalapakati pakati pa Mulungu ndi munthu (1 Timoteo 2:5). Iye yekha ndi munthu amene Mulungu anamukweza: “Mwa icinso Mulungu anamkwezetsa iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse” (Afilipi 2:9).

M’malo ambiri Yesu ananena kuti Iye ndiye njira yopita kumwamba, si pa Yohane 14:6 pokha pamene tipeza mau otero ai. M’malo ena Iye ananeneratu kuti ndiye cikhulupiro pa Mateyu 7:21-27. Iye anatinso kuti mau ace ndi moyo (Yohane 6:63). Iye analonjeza kuti iwo onse wokhulupirira Iye adzakhala ndi moyo wosatha (Yohane 3:14-15). Iye ndiye khomo polowera nkhosa (Yohane 10:7); ndiyenso mkate wa moyo (Yohane 6:35); komanso ndiye kuuka (Yohane 11:25).

Ulaliki wa atumwi unaima kwenikweni pa imfa ndi kuuka kwa Ambuye Yesu. Petro ponena kwa bungwe la oweruza la Sanihedrini, analalikira poyera kuti yesu ndiye njira ya kumwamba: “Ndipo palibe cipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo” (Macitidwe 4:12). Paulo polankhula mu sinagoge ku Antiokeya, ananena bwino kuti Yesu ndiye Mpulumutsi: “Potero padziwike ndi inu amuna abale, kuti mwa iye cilalikidwa kwa inu cikhululukiro ca macimo; ndipo mwa iye yense wokhulupira ayesedwa wolungama” (Macitidwe 13:38-39). Yohane, polembera kwa mpingo wonse, anena kuti cikhululukira ca macimo athu ciri m’dzina la Kristu: “Ndikulemberani, tiana, popeza macimo adakhululukidwa kwa inu mwa dzina lace” (1 Yohane 2:12).

Umoyo wosatha wa kumwamba utheka cabe mwa Yesu Kristu. Yesu anapemphera nati, “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” Kulandira mphatso ya Mulungu ya umoyo wosatha, tiyenera kuayangana kwa Yesu ndi kulunjika kwa yesu yekhayo. Tiyenera kukhulupira mwa imfa ya Yesu kuti Iye anatifera pa mtanda kulipira mlandu wa macimo yathu ndipo anaukitsidwa kwa akufa. “Ndico cilungamo ca Mulungu cimene cicokera mwa cikhulupiriro ca pa Yesu Kristu kwa onse amene akhulupira; pakuti palibe kusiyana” (Aroma 3:22).

Pa nthawi ina yake mu ulaliki wa Yesu, anthu ena ambiri sanamulondole Iye ndipo amayembekezera zopeza mpulumutsi wina. Koma Yesu anafunsa ophunzira ace khumi ndi awiriwo (12), “Kodi mufuna kucoka inunso?” (Yohane 6:67). Ndipo Petro anayankhapo moonadi kuti, “Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nao mau a moyo wosatha. Ndipo 20 ife tikhulupirira, ndipo tidziwa kuti Inu ndinu Woyera wa Mulungu” (Yohane 6:68-69). Tiyeni tonsefe tikhale naco cikhulupiriro monga ca Petro kuti umoyo wosatha upezeka cabe mwa Yesu.

Kodi mwapanga ganizo la Khristu chifukwa cha zimene mwawerenga pano? Ngati ndi choncho, chonde sindikizani batani la “Ndavomera kulandira Khristu lero” pansipa.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi Yesu ndiye njira yokha yopita Kumwamba?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries