Funso
Kodi Baibulo linena ciani za cikwati pakati pa osiyana mitundu (osiyana khungu)?
Yankho
Malamulo a M’cipangano Cakale sanalole Aisrayeli kukwatira anthu amitundu ina (Deuteronomo 7:3-4). Koma kuwaletsa uku sicinali cifukwa ca mtundu wa khungu kapena mtundu ai. Cifukwa, cinali pa za cipembezo. Cifukwa cymene Mulungu anawaletsera iwo kukwatira anthu a mitundu ina ndi cakuti anthuwo anali kupembeza milungu ina yonama. Motero Aisrayeli anayenera kusakwatira mitundu imeneyo kuti asatayike pamaso pa Mulungu ndi kutsata milungu yacikunja. Izi ndizo zinacitika mu Israyeli, monga mwa Malaki 2:11.
Molinganiza ndi zimenezo zokhuza pa ciyero, tizipezanso mu Chipangano Catsopano koma izi sanena za mtundu wina uli wonse: “Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti cilungamo cigawana bwanji ndi cosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?” (2 Akorinto 6:14). Monga momwe Aisrayeli (amene anakhulupira Mulungu m’modzi yekha kukhala woona) analamuliridwa kuti asakwatire opembedza mafano, momwemonso Akristu (amene anakhulupira Mulungu m’modzi yekha kukhala woona) alamuliridwa kuti asakwatire osakhulupira. Baibulo silinena kuti cikwati pakati pa anthu osiyana mitundu ndi coipa ai. Aliyense amene aletsa wina kukwatira cifukwa ca mtundu, akungotero pa zifukwa zake cabe osati monga mwa Mau a Mulungu.
Martin Luther King, Jr., akuti, munthu ayenera kuweruzidwa pa zocita zake osati pa mtundu wa khungu lake. Mu umoyo wa M’kristu musakhale kusankhana kapena kukonderana cifukwa ca mtundu (Yakobo 2:1-10). Baibulo itero kuti pali cabe mtundu m’modzi – mtundu wa anthu ndipo aliyense acokera kwa Adam ndi Hava. Posankha munthu wofuna kukwatira, mkristu ayenera adziwe ngati winayo ndi wobwadwa kwatsopano komanso wokhulupirira mwa Yesu Kristu (Yohane 3:3-5). Cikhulupiriro mwa Yesu, ndiwo mpimo wololedwa ndi Baibulo, osati mtundu wa khungu ai. Kukwatirana kotero (kwa pakati pa anthu osiyana khungu) ndi nzeru ya padera ndipo pafunika pemphero.
Iwo ofuna kukwatirana ayenera kuona pa mbali zambiri. Kusiyana khungu sikuyenera kusalowapo, sikuyenera kukhala ngati mfundo kuti awiriwo akwatirane. Anthu okwatirana pa mitundu yosiyana (osiyana khungu) iwo atha kukumana ndi zambiri zovuta, zosawayenera, ndipo iwo ayenera kuyankhapo moyenera kulingana ndi ciphunzitso ca Baibulo. “Pakuti kulibe kusiyana Myuda ndi Mhelene; pakuti Yemweyo ali Ambuye wa onse, nawacitira zolemera onse amene aitana pa Iye” (Aroma 10:12). Mpingo wopanda sankho la khungu la munthu komanso banja limene iwo asiyana khungu atha kukhala citsanzo cabwino zedi coonetsa umodzi wa Kristu.
English
Kodi Baibulo linena ciani za cikwati pakati pa osiyana mitundu (osiyana khungu)?