Funso
Kodi Baibulo linena ciani pa za kulekana pa banja ndi kukwatiranso kapena kukwatiriwanso?
Yankho
Coyamba, ngakhale munthu atakhala ndi ciganizo cotani pa nkhani ya kutha kwa cikwati, ndikofunikira kukumbukira mau opezeka pa Malaki 2:16, “Pakuti ndidana nako kuleka kumene, ati Yehova Mulungu wa Israyeli, ndi iye wakukuta cobvala cace ndi ciwawa, ati Yehova wa makamu; cifukwa cace sungani mzimu wanu kuti musacite mosakhulupirika” Monga mwa Baibulo, cikwati ndi cokhaliratu, kuzipereka mu umoyo wonse. “Cotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Cifukwa cace ici cimene Mulungu anacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse” (Mateyu 19:6). Mulungu adziwa kale kuti pakuti cikwati ndi ca anthu awiri (mwamuna ndi mkazi) onsewo wocimwa pamaso pace, kulekana kudzakhalakobe. Mu Cipangano Cakale, Mulungu Anaika malamulo kuti ateteze maukwati ndi mabanja makamaka akazi (Deuteronomo 24:1-4). Yesu ananena kuti malamulo amenewa anapatsidwa cifukwa ca kuuma mitima kwa anthu, osati cifukwa cakuti Mulungu anafuna kutero ai (Mateyu 19:8).
Bvuto lalikuru kwenikweni la kulekana pa banja ndi kukwatiranso kapena kukwatiriwanso kuti ngati ndikololedwa monga mwa Baibulo, kuima pa Mau opezeka pa Mateyu 5:32 ndi 19:9. Mau awa akuti, “pa cifukwa cape ca kusakhulupirika kwa m’banja” kapena “kosakhala cifukwa ca cigololo” pa nthawi ya kukhala ba ubwezni. Monga mwa mwambo wa a Yuda, iwo okhala pa ubwenzi kuyembekeza kuti akwatirane anayesedwa ngati okwatirana kale pa nthawi yonseyo yoyembekezera. Ndipo monga mwa mwambo umenewu, ngati wina wa iwo wapezedwa akucita zadama pamenepo ndiko kuti amenewo (oyembekezera kukwatirana) anayenera kulekana.
Koma mau a Cigiriki osanthulitsidwa kuti “kosakhala cifukwa ca cigololo” ndi mau akutanthauza kucita zadama zina zirizonse. Mauwo akhoza kutanthauzanso ciwerewere, uhule, cigololo ndi zina za cilakolako zotero. Yesu pano cioneka kuti akunena kuti kulekana ndikofunika ngati pacitika cimo lotero. Kugona malo amodzi ndi gawo locitidwa ulemu kwambiri m’cikwati: “awiriwo adzakhala thupi limodzi” (Genesis 2:24; Mateyu 19:5; Aefeso 5:31). Motero aliyense amene acita mosasamala kupeleka ulemu kapena kucitira ulemu thupi lace pa gawo cikwati polola kugona ndi wina, ndico cifukwa cimene banja lingathere. Ngati ndi tero, Yesu anaonanso pa gawo la wokwatiransokapena wokwatiriwanso mu mau awa. Mau akapandamneni akuti, “ndi kukwatiranso kapena kukwatiriwanso” (Mateyu 19:9) zionetsa kuti kulekana ndi kukwaatiranso kapena kukwatiriwanso ndi kololedwa pokhapo mbanjalo mukacitika zotero zogona kubwalo kwa banja. Pano ndicofunika kudziwa kuti amene ayenera kapena kuloledwa kukwatiranso kapena kukwatiriwanso ndi iye amene sanagone kubwalo kwa banja (iye amene sanacite cigololo). Ngakhale kuti ndizosachulidwa pa vesi limenelo, kukwatira kapena kukwatiriwanso kwa iye amene sanacimwe kunacitika pa cifundo ca Mulungu cabe, koma mau sakunenanso tero apa. Pakhoza kukhala nthawi zina pamene “wolakwayo” amapatsidwa mpata wakukwatira kapena kukwatiriwanso, koma izi ndizosachulidwa m’mau awa pano.
Ena amavetsa 1 Akorinto 7:15 kukhala “yapadera” kulola kukwatiranso ngati wosakhulupirira walekana ndi wokhulupirira. Koma kuwerenga bwino, pomwepo sanenapo za kukwatiranso koma anena kuti okhulupirika samangidwa kupitiliza mu cikwati ngati wosakhulupirirayo afuna kucoka kapena kuti asiyane. Ena amanena kuti, ngati pakati pabanjalo pali mcitidwe wa nkhanza, ndi njira yololedwa kusiya banja ngakhale kuti Baibulo silinenapo kanthu kotero pamenepo. Zimenezi zikhoza kukhala tero, koma sicinthu ca nzeru kuyamba kuyelekezera kuti Baibulo likadayenera kutero kapena kunenapo kanthu pomwepo.
Nthawi zina sipakhala kumvetsa mau amenewo akuti, “kosakhala cifukwa ca cigololo” atanthauza ciani, imakhala sitepe lodzetsa kulekana, mosakambilana konse ai kapena kumvetsa mauwo. Ngakhale kuti pacitika cigololo, banja kupyolera mwa cisomo ca Mulungu likhoza kukambilana, kuphunzira ndi kukhululukirana ndi kumanga banja lao. Mulungu watikhululukira ife pa zambiri kwambiri koposa zamene ena aticimwira. Ndizoonadi, ife tonse tingathe kulondola citsanzo cake ndi kukhululukira cimo la cigololo (Aefeso 4:32). Koma pali anthu ena m’banja amene mcitidwe wao ndi wosasamala, iwo nthawi zambiri zimapezeka kuti angocita zadamazo mosalemekeza winayo ndi banja. Pamenepo ndiye pamene pamabwerera mau opezeka pa Mateyu 19:9 ndipo atha kugwiritsidwa nchito pamenepo. Anthu ena ambiri akalena ndi amwao, amathamangira kukwatira kapena kukwatiriwa kusadziwa kuti mwina Mulungu afuna kuti iwo akhala tero kopanda mkazi kapena mwamuna. Nthawi zina Mulungu amafuna kuti anthu ena akhale okha monga mwa mau apa (1 Akorinto7:32-35). Kukwatira kapena kukwatiriwanso kumakhala ngati kusankha nthawi zambiri, koma kutero sindiko kunena kuti palibe njira ina ai.
Ndi cinthu cobvutitsa kwambiri kuona kuti ciwerengero ca anthu amene amaitana pa dzina la Kristu amene zikwati zao zkutha, nambala imeneyo ndi yokwera ndithu monga ya iwo wosakhulupirira. Baibulo lineneratu kuti Mulungu adana nako kulekana kwa anthu okwatirana (Malaki 2:16) ndiponso kuti kukambirana ndi kukhululukirana ziyenera kukhala pa mtima pa Mkristu aliyense (Luka 11:4; Aefeso 4:32). Koma Mulungu adziwa kuti kulekana kudzacitikabe ndithu pakati pa ana ake. Munthu wokhulupirira amene walekedwa kapena amene wakwatiranso kapena kukwaririwanso sayenera kumva kapena kuganiza kuti cikondi ca Mulungu pakati pa iye ndi cocepekera kapena cacing’ono, ngakhale kuti iwo wolekedwa kapena iwo okwatiranso kapena wokwatiriwanso sachulidwa pa mau apa Mateyu 19:9. Mulungu amagwiritsa nchito ngakhale mbali ya kusamvera kwa Akristu ocimwa kuti akwaniritse nchit yake yaikulu.
English
Kodi Baibulo linena ciani pa za kulekana pa banja ndi kukwatiranso kapena kukwatiriwanso?