settings icon
share icon
Funso

Kodi malamulo anai a zauzimu ndi otani?

Yankho


Malamulo Anai a Zauzimu ndi njira imodzi yogwiritsa nchito pogawana uthenga wabwino wa cipulumutso copezeka mwa Yesu Kristu. Njira imeneyi imacitidwa mosonkhanitsa mfundo zinai zofunikira kucokera mu Uthenga wabwino.

Coyamba ca Malamulo Anai awa a Zauzimu, “Mulungu akukondani ndipo ali ndi njira ya cipulumutso ca moyo wanu.” Yohane 3:16 anena kuti, “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.” Pa Yohane 10:10 atipatsa cifukwa cymene Yesu anabwerera ku dziko lapansi “Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wocuruka.” Kodi cymene cikutiletsa ife kuyanjana ndi Mulungu ndi ciani? Kodi cymene cikutiletsa ife kukhala ndi moyo wocuruka nciani?

Caciwiri ca Malamulo Anai awa a Zauzimu ndi, “Umunthu wathu ndi waucimo motero sikutheka kuyanjana ndi Mulungu. Pacifukwa ici sitingathe kudziwa za njira ya Mulungu mu miyoyo yathu.” Aroma 3:23 akutero kuti, “pakuti onse anacimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu.” Ndipo pa Aroma 6:23 anena za zotulukamo mu ucimo, “Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” Mulungu anatilenga kuti tikhale m’ciyanjano ndi Iye. Koma ucimo unadza mdziko lapansi ndi kutilekanitsa ndi Mulungu wathu. Taononga ubale wathu umene Mulungu anaupanga kuti ukatithandize. Kodi cotsatira ndi ciani tsopano?

Cacitatu ca Malamulo Anai awa a Zauzimu ndi, “Yesu Kristu ndi yekhayo amene Mulungu anamupereka kucotsa macimo. Kupyolera mwa Yesu Kristu, macimo athu akhululukidwa ndipo Yesu yemweyo alumikiza ubale pakati pa ife ndi Mulungu.” Pa Aroma 5:8 akuti, “Koma Mulungu atsimikiza kwa ife cikondi cace ca mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife cikhalire ocimwa, Kristu adatifera ife.” Pa 1 Akorinto 15:3-4 atiuza kuti tiyenera kudziwa ndi kukhulupirira kuti tipulumutsidwe, “…kuti Kristu anafera zoipa zathu, monga mwa malembo; ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lacitatu, monga mwa malembo…” Yesu mwini ananetsa kuti Iye ndiye njira ya cipulumutso mu Yohane 14:6 “Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.” Kodi ndingalandire bwanji mphatso yabwino yotere yacipulumutso?

Cacinai ca Malamulo Anai awa a Zauzimu ndi, “Tiika cikhulupiriro cathu mwa Yesu Kristu kukhala Mpulumutsi wathu kuti potero tilandire mphatso yaulere yacipulumutso ndi kudziwa cifuniro ca Mulungu pa miyoyo yathu.” Pa Yohane 1:12 pali mau awa, “Koma onse amene anamlandira iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lace.” Ndipo pa Macitidwe 16:31 mau akutere kuti, “Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka!” Tipulumutsidwa mwa chisomo cokha, ndi cikhulupiro cokha, ndi mwa Yesu yekha (Aefeso 2:8-9).

Ngati mufuna kukhulupira Yesu kukhala Mpulumutsi wa moyo wanu, nenani mau awa kwa Mulungu. Kulankhula mau awa sikudzakupulumutsani, koma kukhulupirira Yesu kudzakupulumutsani. Pemphero ili ndi njira cabe yoonetsa kuti cikhulupiriro canu ciri mwa Mulungu ndi kumuyamika Iye popereka cipulumutso kwa inu. “Mulungu, ndidziwa kuti ndakucimwirani ndipo ndiyenera cilango cosatha. Koma Yesu Kristu anatenga cilango cimeneco m’malo mwa ine ndipo mwa Iye yekha ndikhululukidwa macimo anga onse. Ndaika cikhulupiriro canga ndi cipulumutso canga mwa Inu. Zikomo cifukwa ca cisomo canu ndi cikhululukiro ca macimo – cimene ciri mphatso ya moyo wosatha. Amen!”

Kodi mwapanga ganizo la Khristu chifukwa cha zimene mwawerenga pano? Ngati ndi choncho, chonde sindikizani batani la “Ndavomera kulandira Khristu lero” pansipa.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi malamulo anai a zauzimu ndi otani?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries