Funso
Kodi Baibulo linena ciani pa za kuzitema kapena kuzilembalemba mphini pa thupi kapenanso kuziboola pa thupi?
Yankho
Lamulo la M’cipangano Cakale analamulira Aisrayeli motere, “Musamadziceka matupi anu cifukwa ca akufa, kapena kutema mpbini; Ine ndine Yehova” (Levitiko 19:28). Tsopano ngakhale kuti okhulupirira alero samangidwa ndi lamulo la M’cipangano Cakale (Aroma 10:4; Agalatiya 3:23-25; Aefeso 2:15), coonadi ndi cakuti panali lamulo lokhuzana ndi za kuzitema kapena kuzilembalemba mphini pa thupi kapenanso kuziboola pa thupi. Koma Cipangano Catsopano sicinenapo kathu ai kuti kutero ndi koletsedwa kapena ndi kololedwa kuti munthu aziteme kapena kuzilembalemba mphini pa thupi kapenanso kuziboola pa thupi pace.
Mu buku la Petro ndipo pa 1 Petro 3:3-4 tipezapo lamuli ili: “Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kubvala za golidi, kapena kubvala cobvala; koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'cobvala cosaola ca mzimu wofatsa ndi wacete, ndiwo wa mtengo wace wapatali pamaso pa Mulungu.” Kuonapo mwakuya, nkhani imeneyi inena za Mkristu koma wamkazi, komabe pali ciphunzitso pano cymene tiyenera kulingalirapo ndi kulondola: kuzionjezera kapena kuzikometsera kusakhale cinthu cacikulu mu umoyo wa munthu. Anthu ambiri, zambiri zao zikupita ku gawo limeneli, “kukometsa tsitsi” mwa njira zosiyana-siyana, komanso “zobvala” ndi zina mwina zobvala mkosi kapena kumanja zopangidwa mwina ndi zinthu za mtengao wapatali komanso zodula koma kodi zimenezo ndizo zionetsa ukoma kwa mtima wace? Tiyenera kusamala ndithu kukonza za maonekedwa abwino a mkati mwa matupi athupi – tonsefe amuna ndi akazi omwe.
Kunena za kuzitema kapena kuzilembalemba mphini pa thupi kapenanso kuziboola pa thupi, tiyenera kudzifunsa ngati Mulungu angathe kugwiritsa nchito gawo limene monga m’mene ife tafunira. “Cifukwa cace mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale mucita kanthu kena, citani zonse ku ulemerero wa Mulungu” (1 Akorinto 10:31). Cipangano Catsopano sicinena molunjika pa gawo ili la kuzitema kapena kuzilembalemba mphini pa thupi kapenanso kuziboola pa thupi komanso silitipatsa mfundo za kukhulupirira kuti Mulungu watilola ife kuzitema kapena kuzilembalemba mphini pa thupi kapenanso kuziboola pa thupi.
Cacikulu cofunikira kudziwa pa zinthu zimene Baibulo silinenapo kanthu kwenikweni ndi cakuti ngati mukaika ngati cinthuco cikondweretsa Mulungu, simuyenera kucicita cinthuco. Aroma 14:23 atikumbutsa ife kuti ciri conse cymene cibwera kopanda cikhulupiriro ndi cimo. Tiyenekera kukumbukira kuti matupi athu ndiponso miyoyo yathu, yaomboledwa ndipo yali m’manja ya Mulungu. Ngakhale kuti pa 1 Akorinto 6:19-20 sanena molunjika pa nkhani ya kuzitema mphini, koma pamenepo tipezapo ciphunzitso: “Kapena simudziwa kuti thupi lanu liri kacisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Pakuti munagulidwa ndi mtengo wace wapatali; cifukwa cace lemekezani Mulungu m'thupi lanu.” Coonadi cimeneci ciyenera kutithandiza pa zamene timacita ndi kumene timapita ndi matupi athu. Ngati matupi athu ali ace a Mulungu tiyenera kukhala naco cilolezo tisanati tizilembelembe kapena kuzicekacepa mphini.
English
Kodi Baibulo linena ciani pa za kuzitema kapena kuzilembalemba mphini pa thupi kapenanso kuziboola pa thupi?